Kubweleza za m’Sukulu ya Ulaliki
Tidzakambilana mafunso otsatilawa pa Sukulu ya Ulaliki mkati mwa mlungu wa December 30, 2013. Taonetsa deti la mlungu umene tidzaphunzila mfundo iliyonse. Tacita zimenezi kuti mlungu uliwonse tizifufuza mfundozo pokonzekela.
1. N’ciani cingatithandize kukhala ofatsa pocita zinthu ndi akulu-akulu a boma? (Tito 3:2) [Nov. 4, w03 4/1 tsa. 25, ndime 18-19]
2. Kodi tiphunzilapo ciani pa mau a Paulo kwa Filimoni opezeka pa Filimoni 4, 5, ndi 7? [Nov. 4, w08 10/15 tsa. 31 ndime 1, 2; w92 4/15 tsa. 25 ndime 2]
3. Kodi tingaloŵe bwanji mu mpumulo wa Mulungu? (Aheb. 4:9-11) [Nov. 11, w11 7/15 tsa. 28 ndime 16, 17]
4. Kodi timaphunzila ciani kwa Samueli ndi oweluza ndiponso aneneli okhulupilika amene anacita “cilungamo”? (Aheb. 11:32, 33) [Nov. 18, w11 1/1 tsa. 25 ndime 5, 6]
5. N’cifukwa ciani Yakobo analemba kuti “nzelu yocokela kumwamba, coyamba ndi yoyela, kenako yamtendele”? (Yak. 3:17) [Nov. 25, w11 8/15 mas. 30-31 ndime 15]
6. Kodi “uthenga wabwino unalengezedwa” kwa “akufa” ati? (1 Pet. 4:6) [Dec. 2, w08 11/15 tsa. 21 ndime 8]
7. Malinga ndi 1 Yohane 2:7, 8, kodi lamulo “lakale” ndiponso “latsopano” limene Yohane akunena ndi liti? [Dec. 9, w08 12/15 tsa. 27 ndime 6
8. Kodi dzina lakuti “Alefa ndi Omega” ndi lakuti “Woyamba ndi Wotsiliza” ndi la ndani? (Chiv. 1:8, 17) [Dec. 16, w09 1/15 tsa. 30 ndime 6]
9. Kodi Akristu odzozedwa amasindikizidwa cisindikizo m’njila ziŵili ziti? (Chiv. 7:3) [Dec. 23, w07 1/1 tsa. 31 ndime 2]
10. N’cifukwa ciani tingakhale otsimikiza kwambili kuti madalitso onenedwelatu mu ulamulilo wa Ufumu adzakhalakodi? Nanga zimenezi ziyenela kutikhudza bwanji? (Chiv. 21:5, 6) [Dec. 30, re tsa. 304 ndime 9]