Ndandanda ya Mlungu wa January 13
MLUNGU WA JANUARY 13
Nyimbo 131 ndi Pemphelo
□ Phunzilo la Baibo la Mpingo:
jr mutu 3 ndime 1 mpaka 6 (Mph. 30)
□ Sukulu ya Ulaliki:
Kuŵelenga Baibo: Genesis 6–10 (Mph. 10)
Na. 1: Genesis 9:18–29 ndi 10:1-7 (Mph. 4 kapena zocepelapo)
Na. 2: Mmene Mungayankhile Ngati Wina Wanena Kuti, ‘Ngati Umakhulupilila Yesu, Palibe Vuto Ndi Chalichi Cimene Umakapemphelako’—rs tsa. 93 ndime 2 (Mph. 5)
Na. 3: Kodi Mkristu Angathetse Bwanji Cizoloŵezi Coseŵeletsa Malisece?—lv tsa. 218-219 (Mph. 5)
□ Msonkhano wa Nchito:
Nyimbo 69
Mph. 10: Kufunika Kobweleza Mfundo mu Utumiki Wakumunda. Nkhani yocokela m’buku la Sukulu ya Utumiki, patsamba 206 ndi 207. Mwacidule citani citsanzo cimodzi kapena ziŵili pa mfundo za m’nkhaniyi.
Mph. 10: Amuna Otumikila Bwino. (1 Tim. 3:13) Funsani atumiki othandiza aŵili. Kodi ali ndi maudindo otani mumpingo? Nanga maudindo ao aphatikizapo ciani? N’cifukwa ciani anakalamila kukhala atumiki othandiza? N’cifukwa ciani amadzipeleka kutumikila mumpingo ndi kuthandiza akulu? Ngati pampingo wanu palibe atumiki othandiza, kambilanani nkhani yocokela m’buku la Gulu mutu 6, pa kamutu kakuti “nchito zao.”
Mph. 10: “Tengelani Citsanzo kwa Aneneli—Mika.” Mafunso ndi mayankho.
Nyimbo 35 ndi Pemphelo