Ndandanda ya Mlungu wa January 27
MLUNGU WA JANUARY 27
Nyimbo 106 ndi pemphelo
□ Phunzilo la Baibo la Mpingo:
jr mutu 3 ndime 13 mpaka 19 (Mph. 30)
□ Sukulu ya Ulaliki:
Kuŵelenga Baibo: Genesis 17–20 (Mph. 10)
Na. 1: Genesis 17:18–26 ndi 18:1-8 (Mph. 4 kapena zocepelapo)
Na. 2: Yesu Sanapite Kumwamba Ndi Thupi Lanyama—rs tsa. 107 ndime 2 ndi tsa. 108 ndime 2 (Mph. 5)
Na. 3: Kodi Babulo Wamkulu N’ciani?—bh tsa. 219-220 (Mph. 5)
□ Msonkhano wa Nchito:
Nyimbo 121
Mph. 5: Kuyambitsa Phunzilo la Baibo pa Ciŵelu Coyamba. Nkhani. Fotokozani makonzedwe amene apangidwa pampingo olalikila pa Ciŵelu coyamba mu February, ndipo limbikitsani onse kutengako mbali. Citani citsanzo cacidule mwa kugwilitsila nchito ulaliki wacitsanzo uli patsamba 4.
Mph. 15: Kodi Zolinga Zanu Zauzimu N’zotani? Kukambitsilana kocokela m’buku la Gulu, tsamba 117, ndime 2, mpaka kumapeto. Funsani wofalitsa mmodzi kapena aŵili amene anakwanilitsa colinga cao ca utumiki wa nthawi zonse. Kodi analimbikitsidwa bwanji ndi anthu ena? Kodi anagonjetsa zopinga zotani? Nanga ndi madalitso otani amene apeza?
Mph. 10: “Kupelekela Munthu Magazini Kumathandiza Kuyambitsa Maphunzilo a Baibo.” Mafunso ndi mayankho. Pemphani omvela kuti afotokoze mmene anayambitsila phunzilo la Baibo kwa munthu amene anali kumpelekela magazini.
Nyimbo 103 ndi Pemphelo