Ndandanda ya Mlungu wa February 3
MLUNGU WA FEBRUARY 3
Nyimbo 22 ndi Pemphelo
□ Phunzilo la Baibo la Mpingo:
jr mutu 4 ndime 1 mpaka 8 (Mph. 30)
□ Sukulu ya Ulaliki:
Kuŵelenga Baibo: Genesis 21–24 (Mph. 10)
Na. 1: Genesis 23:1-20 (Mph. 4 kapena zocepelapo)
Na. 2: Cifukwa Cimene Yesu Ankavalila Matupi Anyama—rs tsa. 108 ndime 3 mpaka tsa. 109 ndime 2 (Mph. 5)
Na. 3: Khalani Ndi Cikhulupililo Cimene Cimakondweletsa Mulungu—bh tsa. 176 ndime 5-7 (Mph. 5)
□ Msonkhano wa Nchito:
Nyimbo 81
Mph. 10: Kugaŵila Magazini mu February. Kukambilana. Yambani ndi citsanzo coonetsa mmene mungagaŵilile magazini pogwilitsa nchito zitsanzo za ulaliki patsamba limeneli. Pambuyo pake fotokozani zitsanzo za ulaliki mwa kuŵelenga ciganizo cimodzi kapena ziŵili za mbali iliyonse, ndipo pemphani omvela kuti afotokoze colinga cake. Kumbutsani omvela kuti azilankhula m’mau ao-ao ndi kuti angasinthe citsanzo kapena kukonzekela cina. Pomalizila limbikitsani omvela kuti azidziŵa bwino nkhani za m’magazini ndi kutenga mbali mokwanila pa nchito yogaŵila magazini.
Mph. 10: Zosoŵa za pampingo.
Mph. 10: Mudzawazindikila ndi Zipatso Zao. (Mat. 7:16) Makambilano ocokela mu Buku Lapacaka la 2013, tsa. 47, ndime 1-2; ndi tsa. 52, ndime 1, mpaka tsa. 53, ndime 1. Pemphani omvela kufotokoza zimene aphunzilapo.
Nyimbo 25 ndi Pemphelo