Ndandanda ya Mlungu wa April 21
MLUNGU WA APRIL 21
Nyimbo 132 ndi Pemphelo
Phunzilo la Baibulo la Mpingo:
jr mutu 7 ndime 7-13 (Mph. 30)
Sukulu ya Ulaliki:
Kuŵelenga Baibulo: Ekisodo 15-18 (Mph. 10)
Na. 1: Ekisodo 15:20 mpaka 16:5 (Mph. 4 kapena zocepelapo)
Na. 2: Akristu Safunikila Kusunga Sabata—rs tsa. 346 ¶2-3 (Mph. 5)
Na. 3: N’cifukwa Ciani Tiyenela Kuona Moyo Monga Mphatso Yamtengo Wapatali Yocokela kwa Mulungu—bh-tsa. 125-127 ndime 3-5 ndi lv- tsa. 80 ndime 16 (Mph. 5)
Msonkhano wa Nchito:
Nyimbo 27
Mph. 10: Kodi Mwakonzekela Kulimbana Ndi Mayeselo Kusukulu? Nkhani yokambilana. Pemphani omvela kuti afotokoze ena mwa mavuto amene Akristu acinyamata amakumana nao kusukulu. Fotokozani mmene makolo angagwilitsilile nchito buku la Index, mabuku a Zimene Achinyamata Amafunsa, Webu saiti yathu, ndi zofalitsa zina, pa kulambila kwa pabanja kuti akonzekeletse ana ao kulimbana ndi mayeselo amene adzakumana nao ku sukulu. (1 Pet. 3:15) Sankhani nkhani imodzi kapena ziŵili, ndipo fotokozani mfundo zothandiza zimene zikupezeka m’zofalitsa zathu. Pemphani omvela kuti afotokoze zimene anacita kuti athe kulalikila kusukulu.
Mph. 20: Zosoŵa za pampingo.
Nyimbo 125 and Pemphelo