Ndandanda ya Mlungu wa May 12
MLUNGU WA MAY 12
Nyimbo 49 ndi Pemphelo
Phunzilo la Baibulo la Mpingo:
jr mutu 8 ndime 8-13 (Mph. 30)
Sukulu ya Ulaliki:
Kuŵelenga Baibulo: Ekisodo 27-29 (Mph. 10)
Na. 1: Ekisodo 29:19-30 (Mph. 4 kapena zocepelapo)
Na. 2: Yesu Sanagawe Cilamulo ca Mose Kukhala ndi Mbali ya “Mwambo” ndi ya “Makhalidwe Abwino”—rs tsa. 347 ndime 3 mpaka tsa. 348 ndime 1 (Mph. 5)
Na. 3: Kodi Tingatani Kuti Tisiye Kugwilizana ndi Mizimu Yoipa?—bh tsa. 103-104 ndime 14 mpaka 16 (Mph. 5)
Msonkhano wa Nchito:
Nyimbo 75
Mph. 15: Mitundu Yonse Idzakhamukila Kumeneko. (Yes. 2:2) Funsani ofalitsa aŵili, mmodzi akhale amene wakhala m’coonadi zaka zambili ndipo winayo akhale watsopano. N’ciani cinawakopa kuti ayambe kuphunzila coonadi? Kodi ndi mavuto otani amene anakumana nao ndipo anawathetsa bwanji? N’ciani cinawasangalatsa kwambili nthaŵi yoyamba imene anapezeka pamisonkhano yampingo? Kodi amakumbukila ciani nthawi yoyamba imene anapita mu ulaliki? Kodi ofalitsa ena mumpingo anawathandiza bwanji kuti apite patsogolo mwa kuuzimu?
Mph. 15: “Kuongolela Luso Lathu mu Ulaliki—Kukonzekela Mau Athu Oyamba.” Kukambilana. Citani citsanzo cacidule ca mbali ziŵili. Mbali yoyamba ioonetse wofalitsa akugwilitsila nchito mau oyamba osakonzekela bwino ndipo yaciŵili ioonetse mau oyamba okonzedwa bwino. Ngati nthawi ilola fotokozani mfundo zimene zingakhale zothandiza zocokela m’buku la Sukulu ya Utumiki, masamba 215 mpaka 219.
Nyimbo 117 ndi Pemphelo