Zilengezo
◼ Cogaŵila mu May, ndi June: Zimene Baibo Imaphunzitsa M’ceni-ceni kapena kamodzi mwa tumapepala twauthenga utu: Kodi Baibo Mumaiona Bwanji?, Kodi Zinthu Zidzakhala Bwanji Mtsogolo?, Kodi Cofunika N’ciani Kuti Banja Likhale Lamtendele?, Kodi Ndani Maka-Maka Amene Akulamulila Dzikoli?, Kodi Mavuto Adzathadi?, ndi kakuti Kodi N’zoona Kuti Akufa Angakhalenso ndi Moyo? July: Uthenga Wabwino Wocokela Kwa Mulungu. August: Ulaliki wapadela wogaŵila kapepala kauthenga katsopano kolengeza Webu saiti ya jw.org.