Ndandanda ya Mlungu wa June 2
MLUNGU WA JUNE 2
Nyimbo 134 ndi Pemphelo
Phunzilo la Baibulo la Mpingo:
jr mutu 9 ndime 9 mpaka 13 (Mph. 30)
Sukulu ya Ulaliki:
Kuŵelenga Baibulo: Ekisodo 38-40 (Mph. 10)
Na. 1: Ekisodo 40:20-38 (Mph. 4 kapena zocepelapo)
Na. 2: Kodi Sabata Limatanthauza Ciani kwa Akristu?—rs tsa. 349; yakonzedwanso: w11 7/15 tsa. 28 ndime 16-17 (Mph. 5)
Na. 3: Kodi Tingaphunzile Ciani pa Nkhani za Anthu Amene Anaukitsidwa Zopezeka m’Baibulo?—(bh tsa. 70-71 ndime 11 mpaka 15 (Mph. 5)
Msonkhano wa Nchito:
Nyimbo 115
Mph. 10: Kugaŵila Magazini mu June. Kukambilana. Yambani ndi citsanzo ca mmene mungagaŵilile magazini, pogwilitsila nchito maulaliki aŵili acitsanzo amene ali pa tsamba lino. Ndiyeno kambilananinso maulaliki acitsanzo amenewo kuyambila poyamba mpaka pa mapeto. Mwacidule malizani mwa kulimbikitsa onse kuti aziwadziŵa bwino magazini ndipo azitengako mbali mosangalala powagaŵila kwa ena.
Mph. 10: Zosoŵa za pampingo.
Mph. 10: Tinacita Zotani? Kukambilana. Pemphani omvela kuti akambe mapindu amene apeza pogwilitsila nchito mfundo za m’nkhani yakuti “Kuongolela Luso Lathu mu Ulaliki—Kukonzekela Mau Athu Oyamba.” Pemphani omvela kuti afotokoze zocitika zolimbikitsa za mu utumiki.
Nyimbo 44 ndi Pemphelo