Zilengezo
◼ Cogaŵila mu June: Zimene Baibo Imaphunzitsa M’ceni-ceni kapena kamodzi ka tumapepala twauthenga utu: Kodi Baibo Mumaiona Bwanji?, Kodi Zinthu Zidzakhala Bwanji Mtsogolo?, Kodi Cofunika N’ciani Kuti Banja Likhale Lamtendele?, Kodi Ndani Maka-Maka Amene Akulamulila Dzikoli?, Kodi Mavuto Adzathadi?, ndi kakuti Kodi N’zoona Kuti Akufa Angakhalenso ndi Moyo? July: Uthenga Wabwino Wocokela Kwa Mulungu. August: Ulaliki wapadela wogaŵila kapepala kauthenga katsopano kolengeza Webu saiti ya jw.org. September: Magazini a Nsanja ya Mlonda ndi Galamukani!
◼ Kuyambila ndi makalasi amene adzacitika cakumapeto kwa caka ca utumiki ca 2014, Sukulu ya Utumiki wa Upainiya idzayamba kucitika masiku 6 okha, kuyambila pa Mande mpaka pa Ciŵelu.