Ndandanda ya Mlungu wa July 7
MLUNGU WA JULY 7
Nyimbo 99 ndi Pemphelo
Phunzilo la Baibulo la Mpingo:
jr mutu 10 ndime 20 mpaka 27 (Mph. 30)
Sukulu ya Ulaliki:
Kuŵelenga Baibulo: Levitiko 17-20 (Mph. 10)
Na. 1: Levitiko 19:19-32 (Mph. 4 kapena zocepelapo)
Na. 2: Cifukwa Cake Akristu Odzozedwa ndi Mzimu, Kapena Kuti “Oyela Mtima,” Si Opanda Macimo—rs tsa. 334 ndime 3 (Mph. 5)
Na. 3: Zimene Baibulo Limanena pa Nkhani ya Phompho—re tsa. 287-288; rs tsa. 356-357 (Mph. 5)
Msonkhano wa Nchito:
Nyimbo 14
Mph. 10: Gaŵilani Magazini M’mwezi wa July. Kukambilana. Yambani mwa kucita citsanzo coonetsa mmene tingagaŵilile magazini mwa kugwilitsila nchito maulaliki acitsanzo amene ali patsamba lino. Ndiyeno kambilanani maulaliki acitsanzo onse. Malizani mwa kulimbikitsa onse kuŵelenga magazini ndi kutengako mbali ndi mtima wonse powagaŵila.
Mph. 10: Zosoŵa za pampingo.
Mph. 10: Kodi Tinacita Zotani? Nkhani yokambilana. Ikambidwe ndi kalembela. Chulani zimene munacita m’nyengo ya Cikumbutso, ndipo yamikilani mpingo kaamba ka nchitozo. Pemphani omvela kuti afotokoze zimene anasangalala nazo pamene anagaŵila tumapepala toitanila anthu ku Cikumbutso, kapena pamene anali kucita upainiya wothandiza.
Nyimbo 123 ndi Pemphelo