Ndandanda ya Mlungu wa July 21
MLUNGU WA JULY 21
Nyimbo 73 ndi Pemphelo
Phunzilo la Baibulo la Mpingo:
jr mutu 11 ndime 9 mpaka 14 (Mph. 30)
Sukulu ya Ulaliki:
Kuŵelenga Baibulo: Levitiko 25-27 (Mph. 10)
Na. 1: Levitiko 26:1-17 (Mph. 4 kapena zocepelapo)
Na. 2: Kodi Anthu Onse Pomalizila Pake Adzapulumutsidwa?—rs tsa. 95 ndime 1 (Mph. 5)
Na. 3: Mmene Malemba Amasiyanitsila Ngozi Yeniyeni Ndi Zinthu Zadala—lv tsa. 84 ndime 23-25 (Mph. 5)
Msonkhano wa Nchito:
Nyimbo 67
Mph. 10: Timapatsidwa Ulemu Cifukwa ca Khalidwe Lathu Labwino ndi Kusatengako Mbali M’zandale. Nkhani yokambilana yocokela mu Buku Lapacaka la 2014, masamba 120 ndi 149. Pemphani omvela kuti anene zimene aphunzilapo.
Mph. 10: Kodi Mudzacitako Upainiya Wothandiza m’Mwezi wa August? Nkhani. Funsani mafunso ofalitsa aŵili kapena atatu amene aganiza zocita upainiya m’mwezi wa August ngakhale kuti ndi odwala kapena ndi otangwanika ndi zinthu zina. Kodi ndi zinthu ziti zimene aona kuti afunika kusintha n’colinga cakuti akacite upainiya? Pemphani woyang’anila nchito kuti anene makonzedwe a utumiki wa kumunda amene mpingo wapanga m’mwezi wa August.
Mph. 10: “Kodi Yehova Amandiona Bwanji?” Mafunso ndi mayankho.
Nyimbo 65 ndi Pemphelo