Ndandanda ya Mlungu wa July 28
MLUNGU WA JULY 28
Nyimbo 58 ndi Pemphelo
Phunzilo la Baibulo la Mpingo:
jr mutu 11 ndime 15 mpaka 21 (Mph. 30)
Sukulu ya Ulaliki:
Kuŵelenga Baibulo: Numeri 1-3 (Mph. 10)
Na. 1: Numeri 3:21-38 (Mph. 4 kapena zocepelapo)
Na. 2: Anthu a Mitundu Yonse’ Adzapulumuka—rs tsa. 95 ndime 2 (Mph. 5)
Na. 3: Kodi Nkhani Zokhudza Kuimbidwa Mlandu Zinkasamalidwa bwanji Nthawi Imene Malamulo a Aheberi ndiponso a Aroma Ankagwila Nchito?—Lev. 5:1; 24:11-14; Deut. 19:16-19; Mac. 23:30, 35 (Mph. 5)
Msonkhano wa Nchito:
Nyimbo 89
Mph. 10: Kodi Mwakonzekela Kulimbana ndi Mayeselo a Kusukulu? Kukambilana. Pemphani omvela kuti afotokoze mavuto amene Akristu acinyamata amakumana nao ku sukulu. Fotokozani mmene makolo angakonzekeletsele ana ao pogwilitsila nchito Webusaiti yathu ndi zofalitsa zina zimene gulu limatulutsa. (1 Pet. 3:15) Sankhani ciyeso cimodzi kapena ziŵili, ndiyeno fotokozani mfundo zothandiza zimene gulu lakonza. Kenako pemphani omvela kuti anene mmene anakwanitsila kucitila umboni ali ku sukulu.
Mph. 10: Funsani Mafunso Kalembela. Kodi udindo wanu umalowetsamo zotani? Kodi oyanganila tumagulu ndi ofalitsa angakuthandizeni bwanji kupeleka lipoti la mpingo loona ndiponso pa nthawi yake? Kodi lipoti loona limathandiza bwanji akulu, oyanganila dela ndi ofesi ya nthambi popeleka cilimbikitso cofunikila?
Mph. 10: “Tengelani citsanzo kwa Aneneli—Zefaniya.” Mafunso ndi mayankho.
Nyimbo 70 ndi Pemphelo