Ndandanda ya Mlungu wa August 11
MLUNGU WA AUGUST 11
Nyimbo 71 ndi Pemphelo
Phunzilo la Baibulo la Mpingo:
jr mutu 12 ndime 8 mpaka 13 (Mph. 30)
Sukulu ya Ulaliki:
Kuŵelenga Baibulo: Numeri 7-9 (Mph. 10)
Na. 1: Numeri 9:9-23 (Mph. 4 kapena zocepelapo)
Na. 2: Munthu Akapulumutsidwa Sizitanthauza kuti Wapulumutsidwa Nthawi Yonse—rs tsa. 96 ndime 3-6 (Mph. 5)
Na. 3: Kodi Tiziopa Anthu Akufa?—bh tsa.58 ndime 5-6 (Mph. 5)
Msonkhano wa Nchito:
Nyimbo 107
Mph. 5: “1914-2014: Ufumu Wakhala Ukulamulila Kwa Zaka 100!” Nkhani yokambilana. Ŵelengani ndime imene ili pamwamba pa tsamba lino. Mbali za Msonkhano wa Nchito mwezi uno zidzafotokoza kwambili za Ufumu. Fotokozani makonzedwe a mpingo wanu a ulaliki wakumunda.
Mph. 10: “Gwilitsilani Nchito Kapepala Katsopano Konena za Webusaiti Yathu.” Kambilanani zimene zili m’kapepala kameneka. Ndiyeno citani citsanzo coonetsa wofalitsa akugaŵila kapepala kameneka ndiyeno akuonetsa munthuyo kapepala pa jw.org pogwilitsila nchito foni yake yokhala ndi Intaneti kapena kacida kena kake.
Mph. 15: “Kunola Luso Lathu mu Ulaliki—Kulankhula za Ufumu Molimba Mtima.” Nkhani yokambilana. Ofalitsa aŵili acite citsanzo pa zocitika izi: Wofalitsa ali pa mzele m’sitolo. Ndiyeno munthu wina kumbuyo kwake akuŵelenga nyuzipepala ndipo akunena kuti: “Koma zinthu zaipilatu m’dzikoli! Anthu onse amaganiza kuti ali ndi yankho koma zinthu zingoipilaipilabe.” Tsopano wofalitsa akudzilankhulila yekha kuti ‘sindifunika kukhala cete. Ndifunika ndilankhule za Ufumu basi!’ Wofalitsa akuti: “N’zoona zinthu zaipa kwambili. Koma kodi mungakonde kulandila kapepala aka? Kakufotokoza za Webusaiti imene yandithandiza kupeza mayankho pa mafunso ofunika kwambili.” Wofalitsa afotokoze mfundo imodzi ya m’kapepalako, ndipo munthuyo aonetse kuti wacita cidwi.
Nyimbo 92 ndi Pemphelo