Kubweleza za m’Sukulu ya Ulaliki
Tidzakambilana mafunso otsatilawa pa Sukulu ya Ulaliki mkati mwa mlungu wa August 25, 2014.
Kodi lemba la Levitiko 18:3 lingatithandize bwanji kupewa kukhala ndi maganizo olakwika a cabwino ndi coipa? (Aef. 4:17-19) [July 7, w02 2/1 tsa. 29 ndime 4]
Tiphunzilapo ciani pa lamulo lopezeka pa Levitiko 19:2? Nanga n’cifukwa ciani tiyenela kuyesetsa kulimvela? [July 7, w09 7/1 tsa. 9 ndime 5]
Kodi lamulo lakale lokhudza kukunkha limatiphunzitsa ciani? (Lev. 19:9, 10) [July 7, w06 6/15 mas. 22-23 ndime 13]
N’cifukwa ciani tinganene kuti lamulo lakuti “diso kulipila diso” silinali kulimbikitsa mfundo yobwezela? (Lev. 24:19, 20) [July 14, w09 9/1 tsa. 22 ndime 3-4]
Ndi liti pamene kunali kulakwa kwa Mwiisiraeli kupempha ciongoladzanja pa ndalama zimene wabweleketsa wina? Nanga ndi liti pamene kunali kololeka kupempha ciongoladzanja? (Lev. 25:35-37) [July 21, w04 5/15 tsa. 24 ndime 3]
N’cifukwa ciani nthawi zambili Baibulo limangochula mafuko 12 a Isiraeli koma kwenikweni anali mafuko 13? (Num. 1:49, 50) [July 28, w08 7/1 tsa. 21]
Ndi phunzilo lotani lonena za kuganizila okalamba limene tiphunzilapo pa lemba la Numeri 8:25, 26 ponena za nchito yokakamiza? [Aug. 11, w04 8/1 tsa. 25 ndime 1]
Atatuluka mu Iguputo mozizwitsa, n’cifukwa ciani Aisiraeli anayamba kudandaula? Nanga ndi phunzilo lofunika liti limene tikuphunzila pankhani imeneyi? (Num. 11:4-6) [Aug. 18, w95 3/1 tsa. 15-16 ndime 10]
Tiphunzilapo ciani pa zimene Mose anacita Elidadi ndi Medadi atakhala aneneli? (Num. 11:27-29) [Aug. 18, w04 8/1 tsa. 26 ndime 4]
Ndi phunzilo lofunika liti limene tiphunzilapo pa lamulo limene linapatsidwa kwa Aisiraeli lakuti “azisokelela mphonje m’mphepete mwa zovala zao”? (Num. 15:37-39) [Aug. 25, w04 8/1 tsa. 26 ndime 7]