Zocitika Zokhudza Ulaliki
Ndife osangalala kuona kuti ofalitsa ndiponso apainiya akupeleka lipoti la kuculuka kwa tumapepala twauthenga ndi mabulosha amene agaŵila mu ulaliki mwezi uliwonse. M’mwezi wa March 2014, tinali ndi ciŵelengelo capamwamba cokwana 754,535 ca tumapepala twauthenga ndi mabulosha amene anafalitsidwa. Tikuyamikila kwambili nchito imene munagwila! Cifukwa ca khama lanu, tinalinso ndi ciŵelengelo capamwamba ca maulendo obwelelako okwana 1,787,395 amene anapangidwa kwa anthu acidwi. Ndife otsimikiza kuti “Mwini zokolola” adzadalitsa khama lanu lobzala ndi kuthilila mbeu za coonadi kwa anthu acidwi, ndipo adzapitiliza ‘kukulitsa’ mbeuzo.—Mat. 9:38; 1 Akor. 3:6.