Ndandanda ya Mlungu wa October 13
MLUNGU WA OCTOBER 13
Nyimbo 8 ndi Pemphelo
Phunzilo la Baibulo la Mpingo:
jr mutu 14 ndime 20 mpaka 25, ndi bokosi patsamba 148 (Mph. 30)
Sukulu ya Ulaliki:
Kuŵelenga Baibulo: Deuteronomo 4-6 (Mph. 10)
Na. 1: Deuteronomo 4:29-43 (Mph. 4 kapena zocepelapo)
Na. 2: Zimene Anthu Ayenela Kusintha Kuti Asangalatse Mulungu—rs tsa. 181 ndime 3-tsa. 182 ndime 1 (Mph. 5)
Na. 3: Zimene Baibulo Limanena pa Nkhani Yogonana Amuna Kapena Akazi Okhaokha—rs tsa. 180 ndime 5-tsa. 181 ndime 2 (Mph. 5)
Msonkhano wa Nchito:
Nyimbo 92
Mph. 5: Tanthauzo la Kulalikila Modzipeleka. Nkhani yolimbikitsa yofotokoza lemba la 2 Timoteyo 4:2. Gwilitsilani nchito nkhani imene ili mu Nsanja ya Olonda ya March 15, 2012, tsamba 16 ndi 17, ndime 7 mpaka 9.
Mph. 10: N’cifukwa Ciani Tiyenela Kulalikila Modzipeleka? Nkhani yokambidwa ndi mkulu yocokela mu Nsanja ya Olonda ya March 15, 2012, tsamba 15-16, ndime 3 mpaka 6, ndiponso tsamba 18, ndime 14 mpaka 18. Gogomezani mmene kugwilitsila nchito nkhani za mu Utumiki wa Ufumu za mutu wakuti “Kunola Luso Lathu mu Ulaliki” kungatithandizile kulalikila modzipeleka.
Mph. 15: “Gwilitsilani Nchito Mipata Imene Muli Nayo Kufalitsa Uthenga wa Ufumu.” Mafunso ndi mayankho. Pokambilana ndime 3, pemphani omvela kuti afotokoze zocitika mu ulaliki zimene anakumana nazo pocita ulaliki wamwai. Tsilizani mwa kugwilizanitsa nkhani imeneyi ndi lemba la mwezi. Ndiyeno, limbikitsani omvela kuti akaŵelenge nkhani ziŵili za mutu wakuti, “Kukambilana ndi Munthu Wina Nkhani za m’Baibulo,” zimene tidzakambilana mlungu wotsatila pa Msonkhano wa Nchito.
Nyimbo 97 ndi Pemphelo