Ndandanda ya Mlungu wa November 10
MLUNGU WA NOVEMBER 10
Nyimbo 99 ndi Pemphelo
Phunzilo la Baibulo la Mpingo:
jr mutu 15 ndime 13 mpaka 20 (Mph. 30)
Sukulu ya Ulaliki:
Kuŵelenga Baibulo: Deuteronomo 19-22 (Mph. 10)
Na. 1: Deuteronomo 22:20-30 (Mph. 4 kapena zocepelapo)
Na. 2: Mmene Ucimo Umakhudzila Ubwenzi Wathu ndi Mulungu—rs tsa. 361 ndime 1–4(Mph. 5)
Na. 3: Kodi Baibulo Limati Ciani pa Nkhani Yopatukana?—lv tsa. 220 ndime 2-tsa. 221 (Mph. 5)
Msonkhano wa Nchito:
Nyimbo 12
Mph. 10: Funsani Mafunso Woyang’anila Nchito. Kodi kusamalila nchito yanu kumaphatikizapo ciani? Ndi zinthu ziti zimene mumayesetsa kucita mukamacezela kagulu ka ulaliki? Kodi amene ali m’kagulu angacite ciani kuti apindule kwambili ndi kucezetsa kwanu? Mumathandiza bwanji ofalitsa amene akufikilani kuti muwathandize pa mbali inayake ya ulaliki?
Mph. 20: “Kunola Luso Lathu mu Ulaliki—Kuonetsa Anthu Cidwi.” Kukambilana. Pambuyo pa kukambilana nkhaniyi, citani citsanzo ca mbali ziŵili. Mbali yoyamba, wofalitsa asaonetse cidwi kwa munthu amene akumugaŵila cofalitsa ca mwezi umenewo. Koma mbali yaciŵili, wofalitsa aonetse cidwi kwa munthu amene akumugaŵila cofalitsa.
Nyimbo 84 ndi Pemphelo