Ndandanda ya Mlungu wa December 8
MLUNGU WA DECEMBER 8
Nyimbo 6 ndi Pemphelo
Phunzilo la Baibulo la Mpingo:
cl mutu 2 ndime 1 mpaka 11 (Mph. 30)
Sukulu ya Ulaliki:
Kuŵelenga Baibulo: Yoswa 1-5 (Mph. 10)
Na. 1: Yoswa 1:1-18 (Mph. 4 kapena zocepelapo)
Na. 2: Kodi Mzimu Woyela Ndi Ciani?—rs tsa. 319 ndime 2–tsa. 320 ndime 1 (Mph. 5)
Na. 3: Kodi Munthu Angacite Bwanji Cigololo ca Kuuzimu?—lv tsa. 51 mpaka 53 ndime 3-6 (Mph. 5)
Msonkhano wa Nchito:
Lemba la Mwezi: Tulutsani “zabwino” m’cuma cabwino cimene mwapatsidwa.—Mat. 12:35a.
Nyimbo 94
Mph. 10: “‘Zabwino’ Zimene Tilandile Mwezi Uno.” Nkhani. Chulani lemba la mwezi. (Mat. 12:35a) Tinalandila coonadi ca kuuzimu kwa munthu amene anatiphunzitsa coonadi. (Onani Nsanja ya Olonda, April 1, 2002, tsa. 16, ndime 5-7.) Ifenso tiyenela kugaŵana ndi ena zinthu “zabwino” zimenezi. (Agal. 6:6) Conco, thandizani abale kukhala ndi cidwi ndi zinthu “zabwino” zimene tilandile mwezi uno pa Misonkhano ya Nchito. Pamisonkhano imeneyi, tidzathandizidwa kukhala ndi luso lophunzitsa ndiponso tidzaphunzila kuimba nyimbo zatsopano.
Mph. 20: “Kunola Luso Lathu mu Ulaliki—Kuonetsa Mocitila Phunzilo la Baibulo Pogwilitsila Nchito Buku la Zimene Baibo Imaphunzitsa.” Kukambilana. Wofalitsa wocita bwino kapena mpainiya acite citsanzo coonetsa mmene timacitila phunzilo la Baibulo pogwilitsila nchito buku la Zimene Baibo Imaphunzitsa.
Nyimbo 96 ndi Pemphelo