N’cifukwa Ciani Tiyenela Kukhala “Odzipeleka pa Nchito Zabwino”?
Kodi ndinu odzipeleka pa nchito zabwino? Monga ofalitsa Ufumu tili ndi zifukwa zambili zocitila zimenezo. N’cifukwa ciani tikutelo? Tiyeni tikambilane zimene timaŵelenga pa Tito 2:11-14:
Mu vesi 11: Kodi ‘kukoma mtima kwakukulu kwa Mulungu’ n’ciani? Nanga aliyense wa ife wapindula bwanji ndi kukoma mtima kumeneku?—Aroma 3:23, 24.
Mu vesi 12: Kodi taphunzitsidwa motani kaamba ka kukoma mtima kwakukulu kwa Mulungu?
Mavesi 13 ndi 14: Popeza kuti tsopano tayeletsedwa, ndi ciyembekezo cotani cimene tili naco? Ndipo ndi colinga cacikulu citi cimene tayeletsedwela ku dziko limene lili ndi makhalidwe oipa?
Kodi mavesi amenewa akulimbikitsani bwanji kukhala wodzipeleka pa nchito zabwino?