Kubweleza za m’Sukulu ya Ulaliki
Tidzakambilana mafunso otsatilawa pa Sukulu ya Ulaliki mkati mwa mlungu wa April 27, 2015. Taonetsa deti la mlungu umene tidzaphunzila mfundo iliyonse. Tacita zimenezi kuti mlungu uliwonse tizitha kufufuza mfundozo pokonzekela.
Kodi cikondi cosatha n’ciani? Nanga ndi anthu ati makamaka amene tiyenela kuwasonyeza cikondi cotelo? (Rute 1:16, 17) [Mar. 2, w12 7/1 tsa. 26 ndime 6]
N’ciani cinacititsa kuti Rute ayambe kudziŵika monga “mkazi wabwino kwambili”? (Rute 3:11) [Mar. 2, w12 10/1 tsa. 23 ndime 1]
Kodi tingatengele bwanji citsanzo ca Hana pamene takumana ndi mavuto? (1 Sam. 1:16-18) [Mar. 9, w07 3/15 tsa. 16 ndime 4-5]
4. N’ciani cinathandiza Samueli kuti asatengele citsanzo coipa ca ana a Eli pamene iye anali “kukula akukondedwa ndi Yehova”? (1 Sam. 2:21) [Mar. 9, w10 10/1 tsa. 16 ndime 2-3]
Tingaphunzile ciani pa zimene Sauli anacita pokana kucita zinthu mopupuluma pamene “anthu oipa” anakana ufumu wake? (1 Sam. 10:22, 27) [Mar. 23, w05 3/15 tsa. 23 ndime 1]
Kodi tiphunzilapo ciani pa maganizo olakwika a Sauli akuti kupeleka nsembe ndi kofunika kwambili kuposa kumvela Yehova? (1 Sam. 15:22, 23) [Mar. 30, w07 6/15 tsa. 26 ndime 3-4]
N’cifukwa ciani n’zolimbikitsa kudziŵa kuti Yehova ‘amaona mmene mtima wa munthu ulili’? (1 Sam. 16:7) [Apr. 6, w10 3/1 tsa. 23 ndime 7]
8. Malinga ndi lemba la Miyambo 1:4, kodi tili ndi ciani cimene Yehova amayembekezela kuti tizicigwilitsila nchito tikakumana ndi mavuto? (1 Sam. 21:12, 13) [Apr. 13, w05 3/15 tsa. 24 ndime 4]
Pamene Abigayeli anapatsa cakudya Davide ndi anthu ake, n’cifukwa ciani sitinganene kuti iye anali kupandukila mwamuna wake amene anali mutu wa banja? (1 Sam. 25:10, 11, 18, 19) [Apr. 20, w09 7/1 tsa. 20 ndime 3]
Abigayeli anapepesa pa zinthu zimene sanacite. Nanga tingaphunzile ciani pa citsanzo cake? (1 Sam. 25:24) [Apr. 20, w02 11/1 tsa. 5 ndime 1, 4]