Ndandanda ya Mlungu wa April 27
MLUNGU WA APRIL 27
Nyimbo 111 ndi Pemphelo
Phunzilo la Baibulo la Mpingo:
cl mutu 8 ndime 17-24, ndi bokosi pa tsa. 86 (Mph. 30)
Sukulu ya Ulaliki:
Kuŵelenga Baibulo: 1 Samueli 26-31 (Mph. 8)
Kubweleza za m’Sukulu ya Ulaliki (Mph. 20)
Msonkhano wa Nchito:
Lemba la Mwezi: Yendani monga anthu anzelu mwa ‘kugwilitsila nchito bwino nthawi yanu.’—Aef. 5:15, 16.
Nyimbo 66
Mph. 7: Gwilitsilani Nchito Mafunso Kuti Muphunzitse Mogwila Mtima. Nkhani yozikidwa m’buku la Sukulu ya Utumiki, tsamba 239. Citani citsanzo cacidule cosonyeza mfundo imodzi kapena ziŵili za m’nkhaniyi.
Mph. 10: Muzitsimikizila Kuti Zinthu Zofunika Kwambili Ndi Ziti. (Afil. 1:10) Funsani mafunso m’bale mmodzi kapena aŵili amene ndi mitu ya mabanja, amenenso amacita khama mu ulaliki ngakhale kuti ali pa nchito yolembedwa komanso ali ndi udindo waukulu wosamalila banja. Kodi amacita ciani kuti apeze nthawi yopita mu ulaliki ngakhale kuti ndi otangwanika? Nanga ndi mapindu otani amene io ndi banja lao apeza cifukwa ca kucita khama mu ulaliki?
Mph. 13: “Gwilitsilani Nchito Mphamvu ya Mau a Mulungu mu Ulaliki.” Kukambilana. Pambuyo pake mucite citsanzo ca mbali ziŵili. Mbali yoyamba, wofalitsa ayambe kukambilana ndi mwininyumba kabuku ka Uthenga Wabwino mwa kugwila mbali ya mau a pa 2 Timoteyo 3:16, 17 popanda kutsegula Baibulo. Mbali yaciŵili, wofalitsa acitenso citsanzo cimodzimodzi. Koma panthawiyi aŵelenge lemba kucokela m’Baibulo. Pemphani omvela kuti afotokoze cifukwa cake citsanzo caciŵili ndi cogwila mtima kwambili.
Nyimbo 124 ndi Pemphelo