Ndandanda ya Mlungu wa April 20
MLUNGU WA APRIL 20
Nyimbo 24 ndi Pemphelo
Phunzilo la Baibulo la Mpingo:
cl mutu 8 ndime 9-16, ndi bokosi pa tsa. 75 (Mph. 30)
Sukulu ya Ulaliki:
Kuŵelenga Baibulo: 1 Samueli 23-25 (Mph. 8)
Na. 1: 1 Samueli 23:13-23 (Mph. 3 kapena zocepelapo)
Na. 2: N’ciani Cimene Baibulo Limalonjeza Ponena za Mtsogolo?—igw-CIN tsa. 16 1-3 (Mph. 5)
Na. 3: Baruki—Mutu: Tumikilani Yehova ndi Mtima Wonse—w14 1/1 tsa. 19 ndime 11 (Mph. 5)
Msonkhano wa Nchito:
Lemba la Mwezi: Yendani monga anthu anzelu mwa ‘kugwilitsila nchito bwino nthawi yanu.’—Aef. 5:15, 16.
Nyimbo 97
Mph. 15: “Mmene Mungacitile Ulaliki Pogwilitsila Nchito Thebulo Kapena Shelufu ya Zofalitsa.” Kukambilana. Citani citsanzo coonetsa ofalitsa aŵili ali pa thebulo la zofalitsa. Wofalitsa woyamba akungomwetulila pamene munthu akudutsa. Koma pamene munthu wina wafika pafupi, wofalitsa waciŵili akumwetulila ndi kumufunsa funso ndipo mwaubwenzi akuyamba kukambilana naye. Kodi tingagwilitsile nchito bwanji njila imeneyi pocita ulaliki wina uliwonse?
Mph. 15: Kodi Mwakonzekela Kulimbana ndi Mayeselo a Kusukulu? Kukambilana. Pemphani omvela kuti afotokoze mavuto amene Akristu acinyamata amakumana nao ku sukulu. Fotokozani mmene makolo angagwilitsile nchito buku Lofufuzila nkhani, Webusaiti yathu, mabuku a Zimene Achinyamata Amadzifunsa pa kulambila kwa pabanja, kuti athandize ana ao kulimbana ndi mayeselo amene amakumana nao kusukulu komanso kuti azitha kufotokoza zimene amakhulupilila. (1 Pet. 3:15) Sankhani ciyeso cimodzi kapena ziŵili, ndiyeno fotokozani mfundo zothandiza zimene zili m’zofalitsa zathu. Kenako pemphani omvela kuti akambe mmene anakwanitsila kucitila umboni ali ku sukulu. Citani citsanzo coonetsa mmene mwana wa sukulu angafotokezele cikhulupililo cake monga Mkristu pa ziyeso zimene amakumana nazo kaŵilikaŵili ku sukulu.
Nyimbo 89 ndi Pemphelo