Zocitika Zokhudza Ulaliki
Tili ndi zifukwa zambili zokhalila okondwela tikaona lipoti la caka cautumiki ca 2014. Anthu oposa 790,000 anapezeka pa Cikumbutso. Tinali ndi ciwelengelo capamwamba ca ofalitsa okwanila 170,245. Ofalitsa okwanila 28,737 anacita upainiya wokhazikika komanso wothandiza m’mwezi wina. Cosangalatsanso kwambili n’cakuti anthu pafupifupi 1,000 anabwezeletsedwa mumpingo. (Luka 15:32) Ulaliki wa m’mizinda ikuluikulu wakhala ukukopa anthu ambili mwezi ulionse. Pa avaleji zofalitsa zoposa 7,000, zimagaŵilidwa mwezi uliwonse pa malo okwanila 5 mu Lusaka ndipo abale amapanga maulendo obwelelako kwa anthu acidwi ambilimbili kaamba ka ulaliki umenewu. Tikuthokoza kwambili Yehova kaamba kotithandiza ndipo tikuyamikila inu nonse amene mwa cikhulupililo munalengeza “uthenga wabwino waulemelelo.”—2 Akor. 4:4.