Ndandanda ya Mlungu wa June 8
MLUNGU WA JUNE 8
Nyimbo 6 ndi Pemphelo
Phunzilo la Baibulo la Mpingo:
cl mutu 10 ndime 18-21, ndi bokosi pa tsa. 106 (Mph. 30)
Sukulu ya Ulaliki:
Kuŵelenga Baibulo: 2 Samueli 19-21 (Mph. 8)
Na. 1: 2 Samueli 19:24-37 (Mph. 3 kapena zocepelapo)
Na. 2: Mungacipeze Bwanji Cimwemwe? —igw-CIN tsa. 22 ndime 1-3 (Mph. 5)
Na. 3: Kayafa—Mutu: Adani a Coonadi Amene Amapha Atumiki a Mulungu Sadzapambana— w06 1/15 tsa. 12 ndime 4–tsa. 13 ndime 3 (Mph. 5)
Msonkhano wa Nchito:
Lemba la Mwezi: “Kumbukilani masiku akale.”—Deut. 32:7.
Nyimbo 90
Mph. 10: “Kumbukilani Masiku Akale.” Nkhani yozikidwa pa lemba la mwezi. Ŵelengani ndi kukambilana Deuteronomo 4:9 ndi 32:7 komanso Salimo 71:15-18. Fotokozani mmene tingapindulile pokumbukila anthu ndi zocitika za mbili yathu. Limbikitsani ofalitsa kuti nthawi zina akamacita Kulambila kwa Pabanja, azikambilana nkhani zopezeka mu Nsanja ya Mlonda za mutu wakuti, “Za m’Nkhokwe Yathu.” Mwacidule, chulani nkhani za mu Msonkhano wa Nchito za mwezi uno, ndipo fotokozani mmene zikugwilizanilana ndi lemba la mwezi.
Mph. 20: “Kunola Luso Lathu mu Ulaliki—Kuyambitsa Phunzilo la Baibulo Pogwilitsila Nchito Kabuku ka Uthenga Wabwino Wocokela Kwa Mulungu.” Nkhani yokambilana yokambidwa ndi woyang’anila nchito. Chulani lipoti la utumiki wa kumunda la mpingo loonetsa kufunika koyambitsa maphunzilo a Baibulo ambili. Wofalitsa wozoloŵela acite citsanzo ca mmene angayambitsile phunzilo la Baibulo pogwilitsila nchito ulaliki umene uli pa kabokosi. Limbikitsani onse kuyambitsa phunzilo la Baibulo.
Nyimbo 29 ndi Pemphelo