Ndandanda ya Mlungu wa June 15
MLUNGU WA JUNE 15
Nyimbo 77 ndi Pemphelo
Phunzilo la Baibulo la Mpingo:
cl mutu 11 ndime 1-8, Cigawo caciŵili, bokosi pa tsa. 107 (Mph. 30)
Sukulu ya Ulaliki:
Kuŵelenga Baibulo: 2 Samueli 22-24 (Mph. 8)
Na. 1: 2 Samueli 22:21-32 (Mph. 3 kapena zocepelapo)
Na. 2: Kaini—Mutu: Zimene Timacita Tikapatsidwa Uphungu Zimasonyeza Umunthu Wathu—w13 1/1 tsa. 15 ndime 3-5 (Mph. 5)
Na. 3: Cikondi ndi Kumvela Zimabweletsa Cimwemwe—igw-CIN tsa. 22 ndime 4-6 (Mph. 5)
Msonkhano wa Nchito:
Lemba la Mwezi: “Kumbukilani masiku akale.”—Deut. 32:7.
Nyimbo 88
Mph. 12: Ndi Munthu Uti Wochulidwa m’Baibulo Amene Mumakonda? Nkhani ndi kufunsa mafunso. Yambani mwa kufunsa mafunso acicepele aŵili kapena atatu. Kodi ndi munthu uti wochulidwa m’Baibulo amene amakonda? Kodi munthuyo anacita zotani? Nanga angatengele bwanji citsanzo cake? Ngati mungathe kupita pa JW.ORG, pitilizani kufotokoza mmene ana angapindulile ndi makadi a anthu ochulidwa m’Baibulo opezeka pa webusaiti yathu. (Pitani pa BIBLE TEACHINGS > CHILDREN.) Khadi lililonse lili ndi mbili yacidule ya munthuyo ndi cithunzi cake, mapu oonetsa kumene anali kukhala, chati coonetsa kutalika kwa nthawi imene anakhalapo ndi moyo ndi mafunso atatu okhudza munthuyo ndi mayankho ake. Makadi amenewa anawapanga m’njila yakuti tingawatenge pa webusaiti yathu. Koma ngati n’zosatsatheka kupita pa JW.ORG kambilanani nkhani za m’kabuku kakuti Phunzitsani Ana Anu. Limbikitsani makolo kugwilitsila nchito cida cimeneci pophunzitsa ana ao “kukumbukila masiku akale.”—Deut. 32:7.
Mph. 18: “Phunzilani kwa Ofalitsa Amene Atumikila Zaka Zambili.” Nkhani yokambilana. Pokambilana ndime 2, pemphani omvela kuti afotokoze mmene apindulila polalikila ndi ofalitsa amenewa.
Nyimbo 4 ndi Pemphelo