Ndandanda ya Mlungu wa July 27
MLUNGU WA JULY 27
Nyimbo 18 ndi Pemphelo
Phunzilo la Baibulo la Mpingo:
cl mutu 13 ndime 1-10 (Mph. 30)
Sukulu ya Ulaliki:
Kuŵelenga Baibulo: 1 Mafumu 15-17 (Mph. 8)
Na. 1: 1 Mafumu 15:16-24 (Mph. 3 kapena zocepelapo)
Na. 2: Kodi Baibulo Lingathandize Bwanji Akazi?—igw-CIN tsa. 26 ndime 3-4 (Mph. 5)
Na. 3: Davide—Mutu: Acinyamata, Konzekelani Kutumikila Yehova Molimba Mtima—w12 7/15 tsa. 23 ndime 4 (Mph. 5)
Msonkhano wa Nchito:
Lemba la Mwezi: “Pitani mukaphunzitse anthu.”—Mat. 28:19, 20.
Nyimbo 65
Mph. 10: Kodi Mukunola Luso Lanu mu Ulaliki? Kukambilana. Kambilanani ndime yoyamba m’nkhani yopezeka mu Utumiki Wathu wa Ufumu wa February 2014 pa tsamba 1, imene ikufotokoza colinga ca nkhani za mutu wakuti: “Kunola Luso Lathu mu Ulaliki.” Chulani mwacidule mitu ina mu nkhani za m’mbuyomu. Pemphani omvela kuti akambe mmene apindulila ndi nkhani zimenezi. Limbikitsani ofalitsa kuyesetsa kutsatila malingalilo opelekedwa mwezi ulionse mwa kucita zimene zili pa kamutu kakuti: “Yesani Kucita Izi Mwezi Uno.”
Mph. 10: Gwilitsilani nchito kabuku ka “Mfundo za m’Mau a Mulungu”—Kuti Muthandize Ophunzila Baibulo Anu. Kukambilana. Kambilanani mmene tingagwilitsile nchito mbali zotsatilazi, pothandiza ophunzila Baibulo kugwilitsila nchito bwino Baibulo. (1) “Mmene Mungapezele Mavesi m’Baibulo” (2) Funso 19: “Kodi mabuku a m’Baibulo ali ndi uthenga wotani?” (3) Funso 20: “Mungacite ciani kuti mupindule kwambili pamene muŵelenga Baibulo?” Citani citsanzo cacidule coonetsa ofalitsa akukambilana mbali zimenezi ndi wophunzila Baibulo kumapeto kwa phunzilo.
Mph. 10: “Zida Zathu Zophunzitsila.” Mafunso ndi mayankho.
Nyimbo 125 ndi Pemphelo