LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • km 7/15 tsa. 4
  • Zocitika Zokhudza Ulaliki

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Zocitika Zokhudza Ulaliki
  • Utimiki Wathu wa Ufumu—2015
Utimiki Wathu wa Ufumu—2015
km 7/15 tsa. 4

Zocitika Zokhudza Ulaliki

◼ Zocitika Zapadela: Mwezi wa May unali wapadela kwambili m’mbili ya Mboni za Yehova mu Zambia. Ofesi ya Omasulila yoyamba imene inamangidwa ku Kabompo, kumpoto koma ca kumadzulo kwa dzikoli, inapelekedwa kwa Mulungu. Pamalo amenewa pali maofesi ndi nyumba zogona za abale ndi alongo omasulila cinenelo ca Ciluvale. Abale anagwila nchito mwakhama kwambili kupanga mapulani, ndi kugwila nchito yomanga ndipo zimenezi zinatenga zaka zitatu. Abale ndi alongo 30 ocokela ku maiko okwanila 5, ndi enanso a mu dziko lathu, anadzipeleka ndi mtima wonse pa nchitoyi. Abalewa anagwila nchito yomanga imeneyi kwa miyezi yoposa 15 mwa kugwilitsa nchito mphamvu ndi maluso ao.

◼ Ndife okondwa kwambili kukudziŵitsaninso kuti mu mwezi umenewo, Baibulo la dziko latsopano la Malemba Opatulika linatulutsidwa m’cinenelo ca Ciluvale. Kunena zoona, abale ndi alongo a Ciluvale ndi okondwela kwambili kukhala ndi Baibulo lomasulidwa bwino, losavuta kumva, lokhala ndi dzina la Mulungu komanso losavuta kuligwilitsila nchito mu ulaliki. Tiyeni tonse mogwilizana, tipitilize kuphunzitsa anthu a “mtundu uliwonse, cinenelo ciliconse,” kudziŵa za Yehova ndi Ufumu wake.—Chiv. 7:9; Mat. 24:14

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani