Ndandanda ya Mlungu wa August 10
MLUNGU WA AUGUST 10
Nyimbo 61 ndi Pemphelo
Phunzilo la Baibulo la Mpingo:
cl mutu 13 ndime 19-23, ndi bokosi pa tsa. 137 (Mph. 30)
Sukulu ya Ulaliki:
Kuŵelenga Baibulo: 1 Mafumu 21-22 (Mph. 8)
Na. 1: 1 Mafumu 22:13-23 (Mph. 3 kapena zocepelapo)
Na. 2: Mungayandikile Bwanji Mulungu?—igw-CIN tsa. 28 ndime 1-4 (Mph. 5)
Na. 3: Delila—Mutu: Kukonda Kwambili Ndalama Kungacititse Munthu Cinyengo—w12 4/15 tsa. 8 ndime 4 (Mph. 5)
Msonkhano wa Nchito:
Lemba la Mwezi: “Koma ine ndi a m’nyumba yanga, tizitumikila Yehova.”—Yoswa 24:15.
Nyimbo 41
Mph. 10: “Koma Ine ndi a m’Nyumba Yanga, Tizitumikila Yehova.” Nkhani yozikidwa pa lemba la mwezi. Ŵelengani ndi kufotokoza Deuteronomo 6:6, 7; Yoswa 24:15; ndi Miyambo 22:6. Gogomezelani kuti amuna afunika kutsogolela banja lao pa zinthu za kuuzimu. Chulani zida zosiyanasiyana zimene gulu lafalitsa zothandiza mabanja. Chulani nkhani zina za mu Msonkhano wa Nchito za mwezi uno ndipo fotokozani mmene zikugwilizanilana ndi lemba la mwezi.
Mph. 20: “Kunola Luso Lathu mu Ulaliki—Phunzitsani Atsopano.” Kukambilana. Pemphani omvela kuti afotokoze mmene makolo angagwilitsile nchito mfundo za m’nkhaniyi pothandiza ana ao kupita patsogolo mwa kuuzimu. Citani citsanzo coonetsa tate akukonzekela ulaliki ndi mwana wake wamng’ono.
Nyimbo 93 ndi Pemphelo