Ndandanda ya Mlungu wa October 12
MLUNGU WA OCTOBER 12
Nyimbo 48 ndi Pemphelo
Phunzilo la Baibulo la Mpingo:
cl mutu 16 ndime 18-22 ndi bokosi tsa. 167 (Mph. 30)
Sukulu ya Ulaliki:
Kuŵelenga Baibulo: 1 Mbiri 5–7 (Mph. 8)
Na. 1: 1 Mbiri 6:48-60 (Mph. 3 kapena zocepelapo)
Na. 2: Kodi Mpatuko N’ciani? (Mph. 5)
Na. 3: Elihu—Mutu: Mabwenzi Enieni Amakamba Zoona—w09 4/15 tsa. 4 ndime 8 (Mph. 5)
Msonkhano wa Nchito:
Lemba la Mwezi: Khalani “ozikika mozama” ndi ‘okhazikika m’cikhulupililo.’—Akol. 2:6, 7.
Nyimbo 117
Mph. 10: Khalani “Ozikika Mozama” ndi ‘Okhazikika m’Cikhulupililo.’ Nkhani yozikidwa pa lemba la mwezi. Kodi ‘kuzikika mozama’ ndi ‘kukhazikika m’cikhulupililo’ kumatanthauza ciani? Nanga tingacite bwanji zimenezi? (Onani Nsanja ya Olonda ya, June 1, 1998, mas. 10-12.) Ŵelengani ndi kukambilana Akolose 2:6, 7; Aheberi 6:1; ndi Yuda 20, 21. Chulani nkhani zina za mu Msonkhano wa Nchito za mwezi uno, ndipo fotokozani mmene nkhanizo zikugwilizanilana ndi lemba la mwezi.
Mph. 20: “Kunola Luso Lathu mu Ulaliki—Thandizani Ophunzila Kukhala ndi Cizolowezi Cabwino Cophunzila Baibulo.” Kukambilana. Citani citsanzo coonetsa wofalitsa waluso akuthandiza wophunzila Baibulo mmene angagwilitsile nchito LAIBULALE YA PA INTANETI ya Watchtower, kapena Buku Lofufuzila Nkhani poyankha mafunso a m’Baibulo.
Nyimbo 116 ndi Pemphelo