Ndandanda ya Mlungu wa October 19
MLUNGU WA OCTOBER 19
Nyimbo 54 ndi Pemphelo
Phunzilo la Baibulo la Mpingo:
ia mas. 2-3 ndi mau oyamba ndime 1-15. (Mph. 30)
Sukulu ya Ulaliki:
Kuŵelenga Baibulo: 1 Mbiri 8-11 (Mph. 8)
Na. 1: 1 Mbiri 11:15-25 (Mph. 3 kapena zocepelapo)
Na. 2: Eliya—Mutu: Musacepetse Mphamvu ya Pemphelo —w11 7/1 tsa.18-22 (Mph. 5)
Na. 3: Kodi Mkulu wa Angelo Ndani? (Mph. 5)
Msonkhano wa Nchito:
Lemba la Mwezi: Khalani “ozikika mozama” ndi ‘okhazikika m’cikhulupililo.’—Akol. 2:6, 7.
Nyimbo 83
Mph. 20: “Mmene Tingaphunzitsile Ena Mowafika Pamtima.” Mafunso ndi mayankho. Citani zitsanzo ziŵili zosiyana. Mwininyumba akuuza wofalitsa kuti mwana wake anamwalila ndipo anapita kumwamba. M’citsanzo coyamba, wofalitsa afotokoza mmene akufa alili mwa kuŵelenga Mlaliki 9:5. Mwininyumba sakutonthozedwa ndi mau apa lembali ndipo sakuonetsa cidwi. M’citsanzo caciŵili, mozindikila, wofalitsa afotokozela mwininyumba za ciyembekezo ca kuuka kwa akufa. Iye aŵelenga Yohane 5:28, 29 ndipo mwininyumba akucita cidwi ndi nkhaniyo.
Mph. 10: Khalani Citsanzo Cabwino kwa Ena Kaya Ndinu Wacinyamata Kapena Wacikulile. (Afil. 3: 17; 1 Tim. 4: 12) Kukambilana kocokela mu Buku Lapacaka la 2015 tsamba 71 ndime 2, mpaka tsamba 72 ndime 4; ndi masamba 76-77. Pemphani omvela kuti akambe zimene aphunzilapo.
Nyimbo 90 ndi Pemphelo