Ndandanda ya Mlungu wa November 16
MLUNGU WA NOVEMBER 16
Nyimbo 17 ndi Pemphelo
Phunzilo la Baibulo la Mpingo:
ia mutu 2 ndime 13-23, ndi kubwelelamo pa tsa. 24 (Mph. 30)
Sukulu ya Ulaliki:
Kuŵelenga Baibulo: 1 Mbiri 26-29 (Mph. 8)
Na. 1: 1 Mbiri 29:20-30 (Mph. 3 kapena zocepelapo)
Na. 2: Kodi “Nsembe Yophimba Macimo” Imatanthauza Ciani? (Mph. 5)
Na. 3: Elizabeti—Mutu: Muziopa Mulungu ndi Kupewa Zoipa—w11 1/15 tsa. 13-14 ndime 5-7 (Mph. 5)
Msonkhano wa Nchito:
Lemba la Mwezi: “Ineyo ndinabzala, Apolo anathilila, koma Mulungu ndiye anakulitsa.”—1 Akor. 3:6.
Nyimbo 35
Mph.10: Pitilizani Kukulitsa Cidwi ca Anthu Amene Mumalalikila. (1 Akor. 3:6-8) Funsani mafunso mpainiya wa nthawi zonse ndi wofalitsa. Kodi anapanga bwanji ndandanda yocita maulendo obwelelako? Nanga amakonzekela bwanji? Kodi amacita bwanji akapeza kuti munthu amene analalikila pa ulendo woyamba sali panyumba? Nanga ndi madalitso otani amene io apeza?
Mph.20: “Mmene Tingagwilitsile Nchito Zinthu Zongomvetsela za pa jw.org.” Mafunso ndi mayankho. Fotokozani mmene ofalitsa angapezele zinthu zongomvetsela za pa jw.org. Lizani nkhani imodzi monga citsanzo ku gulu. Ndiyeno, citani citsanzo ca cocitika cimene cili kumapeto kwa nkhani yakuti “Gwilitsilani Nchito Webusaiti Yathu mu Ulaliki—‘Kuyankha Mafunso a m’Baibulo,’” mu Utumiki Wathu wa Ufumu wa November 2014.
Nyimbo 108 ndi Pemphelo