Ndandanda ya Mlungu wa November 30
MLUNGU WA NOVEMBER 30
Nyimbo 94 ndi Pemphelo
Phunzilo la Baibulo la Mpingo:
ia mutu 3 ndime 14-21, ndi bokosi pa tsa. 30, ndiponso kubwelelamo pa tsa. 32 (Mph. 30)
Sukulu ya Ulaliki:
Kuŵelenga Baibulo: 2 Mbiri 6-9 (Mph. 8)
Na. 1: 2 Mbiri 6:22-27 (Mph. 3 kapena zocepelapo)
Na. 2: Kodi Kupulupudza Kwamwano N’koipa Motani? (Mph. 5)
Na. 3: Epafura—Mutu: Muzitumikila Abale Anu ndi Kuwapemphelela—w13 11/15 tsa. 6 ndime 15 (Mph. 5)
Msonkhano wa Nchito:
Lemba la Mwezi: “Ineyo ndinabzala, Apolo anathilila, koma Mulungu ndiye anakulitsa.”—1 Akor. 3:6.
Nyimbo 58
Mph.10: Kugaŵila magazini mu December. Kukambilana. Yambani mwa kucita zitsanzo ziŵili poseŵenzetsa maulaliki acitsanzo patsamba lino. Ndiyeno, kambilanani maulaliki onse acitsanzo.
Mph.10: Zosoŵa za Pampingo.
Mph.10: Tinacita Zotani? Kukambilana. Pemphani omvela kuti akambe mapindu amene apeza pogwilitsila nchito mfundo za m’nkhani yakuti, “Kunola Luso Lathu mu Ulaliki—Kugaŵila Buku la Zimene Baibo Imaphunzitsa.” Ndiyeno, apemphani kuti afotokoze zocitika zosangalatsa za mu ulaliki.
Nyimbo 141 ndi Pemphelo
Cikumbutso: Lizani nyimbo yatsopanoyo kamodzi, kenako mpingo uimbile pamodzi nyimboyo.