Ndandanda ya Mlungu wa December 28
MLUNGU WA DECEMBER 28
Nyimbo 79 ndi Pemphelo
Phunzilo la Baibulo la Mpingo:
ia mutu 5 ndime 14-26, ndi kubwelelamo pa tsa. 50 (Mph. 30)
Sukulu ya Ulaliki:
Kuŵelenga Baibulo: 2 Mbiri 25-28 (Mph. 8)
Kubweleza za m’Sukulu ya Ulaliki (Mph. 20)
Msonkhano wa Nchito:
Lemba la Mwezi: “Tiyenela kukumana ndi masautso ambili kuti tikaloŵe mu Ufumu wa Mulungu.”—Machitidwe 14:22.
Nyimbo 122
Mph.15: Muzipemphelela Abale Anu. Kukambilana. Yambani ndi kuŵelenga Machitidwe 12:1-11. Ndiyeno, kambilanani mfundo zofunika za m’buku la Kucitira Umboni masamba 77-80, ndime 5-12. Pambuyo pake, ngati mumapita pa Intaneti, chulani nkhani zaposacedwapa zopezeka pa jw.org. Pitani polemba kuti “Malo a Nkhani” (Newsroom). Limbikitsani onse kuti azipemphelela abale amene akukumana ndi mayeselo osiyanasiyana padziko lonse. Ndipo ngati n’kotheka, azichula maina a abalewo m’mapemphelo ao.—2 Akor. 1:11; 1 Tim. 2:1, 2.
Mph.15: Zosoŵa za Pampingo.
Nyimbo 124 ndi Pemphelo