January 4-10
2 MBIRI 29–32
Nyimbo 114 ndi Pemphelo
Mau Oyamba (Mph. 3)
CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU
“Kulambila Koona Kumafuna Kugwila Nchito Mwakhama”: (Mph. 10)
2 Mbiri 29:10-17—Hezekiya abwezeletsa kulambila koona molimba mtima
2 Mbiri 30:5, 6, 10-12—Hezekiya aitana anthu onse a mtima wabwino kuti adzalambile Mulungu
2 Mbiri 32:25, 26—Hezekiya asiya kudzikuza ndipo akhala wodzicepetsa (w05-CN 10/15 tsa. 25 ndime 20)
Kufufuza Cuma Cakuuzimu (Mph. 8)
2 Mbiri 29:11—N’cifukwa ciani Hezikiya ndi citsanzo cabwino pankhani yosankha zinthu zofunika kwambili? (w13-CIN 11/1 tsa. 18 ndime 6-7)
2 Mbiri 32:7, 8—Ndi cinthu canzelu citi cimene tiyenela kucita pokonzekela mavuto a mtsogolo? (w13-CIN 11/1 tsa. 21 ndime 17)
Kodi kuŵelenga Baibulo kwa mlungu uno kundiphunzitsa ciani za Yehova?
Ndi mfundo ziti pa kuŵelenga Baibulo kwa mlungu uno zimene ndingagwilitsile nchito mu ulaliki?
Kuŵelenga Baibulo: 2 Mbiri 31:1-10 (Mph. 4 kapena zocepelapo)
KUONJEZELA LUSO LANU MU ULALIKI
Konzekelani Maulaliki a Mwezi Uno: (Mph. 15) Nkhani yokambilana. Onetsani vidiyo yoonetsa ofalitsa akugaŵila Nsanja ya Mlonda, kenako kambilanani mfundo zimene zili mu vidiyoyo. Gogomezelani mmene wofalitsa ayalila maziko a ulendo wobwelelako. Citaninso cimodzimodzi ndi Galamukani! ndiponso kabuku ka Uthenga Wabwino. Gwilitsilani nchito mfundo zili pa mutu wakuti “Mmene Tingatsogozele Phunzilo m’Kabuku ka Uthenga Wabwino.” Limbikitsani ofalitsa kulemba ulaliki wao pa danga limene lili patsamba loyamba.
UMOYO WATHU WACIKRISTU
“Mwai Womanga ndi Wokonza Malo Athu Olambilila”: (Mph. 15) Nkhani yokambilana. Pemphani amene agwilapo nao nchito yomanga Nyumba za Ufumu kuti afotokoze cisangalalo cimene apeza pogwila nchitoyo. Mwacidule funsani m’bale amene amayang’anila nchito yoyeletsa ndi kukonza Nyumba ya Ufumu kuti afotokoze makonzedwe amene mpingo wanu uli nao pa nchito imeneyi.
Phunzilo la Baibulo la Mpingo: ia Mutu 6 ndime 1-14 (Mph. 30)
Kubweleza Mfundo Zimene Taphunzila ndi kufotokoza Zomwe Tidzaphunzila Mlungu wamaŵa (Mph. 3)
Nyimbo 142 ndi Pemphelo
Cikumbutso: Lizani nyimbo yonse kamodzi, kenako mpingo uimbile pamodzi nyimbo yatsopanoyo.