March 21-27
YOBU 6-10
Nyimbo 68 ndi Pemphelo
Mau Oyamba (Mph. 3 kapena zocepelapo)
CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU
“Munthu Wokhulupilika Yobu Afotokoza Mavuto Ake”: (Mph. 10)
Yobu 6:1-3, 9, 10, 26; 7:11, 16—Zimene anthu amakamba akakumana ndi mavuto si zimene zimakhala mumtima mwao (w13–CIN 8/1 19 ndime 7; w13–CN 5/15 22 ndime 13)
Yobu 9:20-22—Yobu anaganiza molakwika n’kumaona kuti Mulungu analibe nazo nchito zakuti iye ndi munthu wokhulupilika (w15–E 7/1 12 ndime 2)
Yobu 10:12—Ngakhale pamene anakumana ndi mavuto, Yobu anakambabe zabwino za Yehova (w09–CN 4/15 7 ndime 18; w09–CN 4/15 10 ndime 13)
Kufufuza Cuma Cakuuzimu: (Mph. 8.)
Yobu 6:14—Kodi Yobu anaonetsa bwanji kufunika kwa kukoma mtima? (w10–CN 11/15 32 ndime 20)
Yobu 7:9, 10; 10:21—Ngati Yobu anali ndi ciyembekezo cakuti adzaukitsidwa mtsogolo, n’cifukwa ciani anakamba mau a m’mavesi amenewa? (w06–CN 3/15 14 ndime 11)
Kodi kuŵelenga Baibulo kwa mlungu uno kwandiphunzitsa ciani za Yehova?
Ndi mfundo ziti pa kuŵelenga Baibulo kwa mlungu uno zimene ndingagwilitsile nchito mu ulaliki?
Kuŵelenga Baibulo: Yobu 9:1-21 (Mph. 4 kapena zocepelapo)
KUONJEZELA LUSO LANU MU ULALIKI
Ulendo Woyamba: Nsanja ya Mlonda yogaŵila ya 2016 Na. 2 tsa. 16. Chulani za copeleka. (Mph. 2 kapena zocepelapo)
Ulendo Wobwelelako: Nsanja ya Mlonda yogaŵila ya 2016 Na. 2 tsa. 16. Yalani maziko a ulendo wina wobwelelako. (Mph. 4 kapena zocepelapo)
Phunzilo la Baibulo: fg phunzilo 2 ndime 6-8 (Mph. 6 kapena zocepelapo)
UMOYO WATHU WACIKRISTU
Khalani Ozindikila Potonthoza Ena: (Mph. 15) Kukambilana. Onetsani vidiyo imene akulu anaonelela pa sukulu yao ya posacedwapa. Ngati n’zosatheka kuonelela vidiyo akulu awili acite citsanzo ca ulendo waubusa pogwilitsila nchito mfundo zili pa kamutu kakuti “Malingalilo Ena Othandiza” m’kabuku kakuti Munthu Amene Mumakonda (we–CN tsa 18) Ndiyeno, pemphani omvela kuti akambepo pa citsanzo cabwino cimene abale aŵili aonetsa ca mmene tingalimbikitsile munthu amene akuvutika cifukwa ca imfa ya wokondedwa wake.
Phunzilo la Baibulo la Mpingo: ia mutu 11 ndime 12-20, ndi kubwelelamo pa tsa. 98 (Mph. 30)
Kubweleza Mfundo Zimene Taphunzila ndi Kufotokoza Zimene Tidzaphunzila Mlungu Wotsatila (Mph. 3)
Nyimbo 27 ndi Pemphelo