CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU | YOBU 6-10
Munthu Wokhulupilika Yobu Afotokoza Mavuto Ake
Yobu anakhala wosauka, wofedwa, ndipo anadwala kwambili, koma anakhalabe wokhulupilika. Conco, Satana anayesa kumufooketsa kuti asiye kukhala wokhulupilika. “Anzake” atatu a pamtima anabwela kwa iye. Poyamba anaonetsa cifundo. Iwo anakhala ndi Yobu kwa masiku 7 osakamba ngakhale mau amodzi omulimbikitsa. Koma mau amene anakamba pambuyo pake, anali omuimba mlandu okhaokha.
Yobu anakhalabe wokhulupilika kwa Yehova ngakhale anakumana ndi mavuto ambili
6:3; 7:16; 9:20-22; 10:1, 12
Cisoni cinacititsa Yobu kukhala ndi maganizo olakwika. Iye anaganiza molakwika n’kumaona kuti Mulungu analibe nazo nchito zakuti iye ndi munthu wokhulupilika
Cifukwa cofooka ndi mavuto, Yobu sanadziŵe zimene zinali kucititsa mavuto ake
Ngakhale kuti Yobu anali ndi cisoni cacikulu, anauza anthu amene anali kumutsutsa kuti iye anali kukonda Yehova