CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU | MASALIMO 87–91
Khalanibe m’Malo Otetezeka a Wam’mwambamwamba
“Malo Otetezeka” a Yehova amatithandiza kukhala otetezeka mwauzimu
91:1, 2, 9-14
Kuti tikhale m’malo otetezeka a Yehova, tifunika kudzipeleka ndi kubatizika
Amene sakhulupilila Mulungu, sawadziŵa malo otetezeka amenewa
Amene ali m’malo otetezeka a Yehova, salola kuti munthu wina kapena cinthu cina ciwalepheletse kukhulupilila Mulungu kapena kumukonda
“Wosaka mbalame” amachela misampha kuti atigwile
91:3
Mbalame n’zocenjela, ndipo n’zovuta kuzigwila
Wosaka mbalame amaona mmene mbalame zimacitila zinthu, ndipo amapeza njila yozigwilila
Satana, amene ndi “wosaka mbalame,” amaona zimene atumiki a Yehova amacita, ndipo amachela misampha kuti awaononge mwauzimu
Misampha inayi yowononga imene Satana amaseŵenzetsa:
Kuwopa Anthu
Kukonda Cuma
Zosangulutsa Zoipa
Mikangano