February 26–March 4
MATEYU 18-19
Nyimbo 121 na Pemphelo
Mau Oyamba (3 min. olo kucepelapo)
CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU
“Muzisamala Kuti Musadzipunthwitse Kapena Kupunthwitsa Ena”: (10 min.)
Mat. 18:6, 7—Sitiyenela kupunthwitsa ena (“cimwala ca mphelo . . . cimene bulu amayendetsa,” “zopunthwitsa,” “Cimwala ca mphelo,” “Mwala wa Mphelo wa Pamwamba na wa Pansi” nwtsty mfundo zounikila pa Mat. 18:6, 7 na zithunzi)
Mat. 18:8, 9—Tiyenela kupewa ciliconse cimene cingatipangitse kupunthwa (nwtsty mfundo younikila, “Gehena”)
Mat. 18:10—Yehova amadziŵa tikapunthwitsa ena (“amaona nkhope ya Atate wanga” nwtsty mfundo younikila; w10 11/1 peji 16)
Kufufuza Cuma ca Kuuzimu: (8 min.)
Mat. 18:21, 22—Kodi tiyenela kukhululukila m’bale wathu nthawi zingati? (“nthawi 77” nwtsty mfundo younikila pa Mat. 18:22)
Mat. 19:7—Kodi colinga ca ‘kalata yothetsa cikwati’ cinali ciani? (“kalata yothetsa cikwati” nwtsty mfundo younikila pa Mat. 19:7 na zithunzi)
Kodi imwe pacanu, kuŵelenga Baibo kwa wiki ino kwakuphunzitsani ciani za Yehova?
Ni cuma ca kuuzimu cina citi cimene mwapeza pa kuŵelenga Baibo kwa wiki ino?
Kuŵelenga Baibo: (4 min. olo kucepelapo) Mat. 18:18-35
CITANI KHAMA PA ULALIKI
Ulendo Wobwelelako Waciŵili: (3 min. olo kucepelapo) Seŵenzetsani makambilano a citsanzo.
Ulendo Wobwelelako Wacitatu: (3 min. olo kucepelapo) Sankhani mwekha lemba na kugaŵila cofalitsa cophunzitsila Baibo.
Phunzilo la Baibo: (6 min. olo kucepelapo) bhs peji 26 mapa. 18-20—Onetsani mmene mungamufikile pamtima.
UMOYO WATHU WACIKHRISTU
Musakhale Cokhumudwitsa (2 Akor. 6:3): (9 min.) Tambitsani vidiyo.
Kampeni Yoitanila Anthu Ku Cikumbutso Idzayamba pa March 3: (6 min.) Nkhani yozikidwa pa Kabuku ka Umoyo na Utumiki ka February 2016 peji 8. Gaŵilani kapepa koitanila anthu ku cikumbutso kwa aliyense m’gulu, na kukambilana zimene zilimo. Gogomezani kuti nkhani yapadela ya mutu wakuti, “Kodi Yesu Khristu Ndani Maka-maka?” idzakambiwa wiki ya March 19, 2018. Nkhaniyi idzatithandiza kuyembekezela mwacidwi tsiku la Cikumbutso. Fotokozani zimene mpingo wakonza kuti ukathe kufola gawo lonse.
Phunzilo la Baibo la Mpingo: (30 min.) jy mutu 10, na bokosi pa peji 28
Kubwelelamo na Kuchulako za Wiki Yotsatila (3 min.)
Nyimbo 133 na Pemphelo