LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • mwb18 February tsa. 7
  • Kunola Luso Lathu mu Ulaliki—Kuseŵenzetsa Mafunso Mwaluso

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Kunola Luso Lathu mu Ulaliki—Kuseŵenzetsa Mafunso Mwaluso
  • Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2018
  • Nkhani Zofanana
  • Gwilitsilani Nchito Mafunso
    Citani Khama pa Kuŵelenga na Kuphunzitsa
  • Kodi Baibo Ingakuthandizeni Bwanji pa Umoyo Wanu?
    Kondwelani Na Moyo Kwamuyaya!—Maphunzilo a Baibo Okambilana Komanso Zocita
  • Kodi Baibo Ingakuthandizeni Bwanji pa Umoyo Wanu?
    Kondwelani Na Moyo Kwamuyaya!—Maphunzilo a Baibo Oyambilapo
  • Zimene Tiyenela Kupewa Pocititsa Phunzilo la Baibulo
    Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Msonkhano (2016)
Onaninso Zina
Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2018
mwb18 February tsa. 7

UMOYO WATHU WACIKHRISTU

Kunola Luso Lathu mu Ulaliki—Kuseŵenzetsa Mafunso Mwaluso

CIFUKWA CAKE N’KOFUNIKA: Ngati “maganizo a mumtima mwa munthu ali ngati madzi akuya,” ndiye kuti mafunso ali ngati cikopo cowatapila. (Miy. 20:5) Mafunso amacititsa omvela kukambapo maganizo awo. Mayankho a mafunso okonzewa bwino, nthawi zambili amatithandiza kudziŵa maganizo a munthu. Yesu anaseŵenzetsa mafunso mwaluso. Tingatengele bwanji citsanzo cake?

Yesu afunsa funso wophunzila wake

MMENE TINGACITILE:

  • Muzifunsa mafunso akuti muganiza bwanji. Yesu anafunsa ophunzila ake mafunso otsatizana kuti adziŵe maganizo awo. (Mat. 16:13-16; be peji 238 mapa. 3-5) Ni mafunso ati amene mungafunse womvela kuti akambe maganizo ake?

  • Muzifunsa mafunso othandizila. Yesu pofuna kuwongolela maganizo a Petulo, anafunsa mafunso na kupeleka mayankho othekela kuti Petulo aganizile yankho lolondola. (Mat. 17:24-26) Ni mafunso ati othandizila amene mungafunse kuti munthu apeze yankho lolondola?

  • Muzimuyamikila womvela wanu. Pamene mlembi ‘anayankha mwanzelu,’ Yesu anamuyamikila. (Maliko 12:34) Kodi imwe mungati ciani kwa munthu amene wayankha bwino funso?

Muzikhala aulemu. Ise tilibe ulamulilo monga umene Yesu anali nawo. Conco, tiyenela kulemekeza anthu, maka-maka acikulile, amene sitiŵadziŵa, na amene ali na ulamulilo.—1 Pet. 2:17.

TAMBANI MBALI YOYAMBA YA VIDIYO YAKUTI GWILANI NCHITO IMENE YESU ANAGWILA—PHUNZITSANI, NDIYENO, YANKHANI MAFUNSO AYA:

  • N’cifukwa ciani citsanzo ici ca kaphunzitsidwe si cabwino olo kuti uthenga unali wolondola?

  • N’cifukwa ciani sitifunika kufotokoza uthenga cabe?

TAMBANI MBALI YACIŴILI YA VIDIYOYI, NDIYENO YANKHANI MAFUNSO AYA:

  • Kodi m’bale anali kufunsa bwanji mafunso mwaluso?

  • Ni mbali zina ziti za kaphunzitsidwe kake zimene tingatengeleko?

Munthu akudabwa cifukwa cosaphunzitsidwa mwaluso; munthu wazindikila coonadi cifukwa cophunzitsidwa mwaluso

Kodi kaphunzitsidwe kathu kangawakhudze bwanji anthu ena? (Luka 24:32)

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani