LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • mwbr18 May masa. 1-3
  • Malifalensi a Kabuku ka Umoyo na Utumiki Wathu

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Malifalensi a Kabuku ka Umoyo na Utumiki Wathu
  • Malifalensi a kabuku ka Umoyo na Utumiki Wathu (2018)
  • Tumitu
  • MAY 7-13
  • MAY 14-20
  • MAY 21-27
  • MAY 28–JUNE 3
Malifalensi a kabuku ka Umoyo na Utumiki Wathu (2018)
mwbr18 May masa. 1-3

Malifalensi a Kabuku ka Umoyo na Utumiki Wathu

MAY 7-13

CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU | MALIKO 7-8

“Nyamula Mtengo Wako Wozunzikilapo na Kunditsatila Mosalekeza”

nwtsty mfundo younikila pa Maliko 8:34

adzikane yekha: Kapena kuti “aleke kudziona ngati wa iye yekha.” Izi zitanthauza kuti munthuyo ni wokonzeka kudziika m’manja mwa Mulungu kothelatu kapena kuti kudzipeleka kwathunthu kwa iye. Mpake kuti mau a Cigiriki pa vesiyi anamasulidwa kuti “adzikane yekha,” cifukwa kudzikana kungaphatikizepo kuleka kucita zofuna zako, zolinga zako kapena zimene umakonda. (2 Akor. 5:14, 15) Maliko anaseŵenzetsa liu la Cigiriki limodzi-modzi pokamba zakuti Petulo anakana Yesu.—Maliko 14:30, 31, 72.

MAY 14-20

CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU | MALIKO 9-10

“Masomphenya Olimbitsa Cikhulupililo”

nwtsty mfundo younikila pa Maliko 9:7

mau: Mabuku a Uthenga wabwino aonetsa kuti Yehova anakamba mwacindunji na anthu katatu. Aka kanali kaciŵili.—Onani mfundo zounikila pa Maliko 1:11; Yoh. 12:28

Kufufuza Cuma ca Kuuzimu

nwtsty mfundo zounikila pa Maliko 10:17, 18

Mphunzitsi Wabwino: Mwacionekele mwamunayu anaseŵenzetsa mau akuti “Mphunzitsi Wabwino” monga dzina la ulemu, cifukwa nthawi zambili atsogoleli a cipembedzo anali kulamula anthu kuti aziwapatsa ulemu waconco. Olo kuti Yesu sanali kukana kuchulidwa kuti “Mphunzitsi” kapena “Ambuye” (Yoh. 13:13), iye anapeleka ulemu wonse kwa Atate wake.

Palibe wabwino, koma Mulungu yekha: Apa Yesu anaonetsa kuti Yehova ndiye woyenelela kwambili kuika miyezo ya cabwino, ndipo ndiye Yekha amene ali na ulamulilo wosankha cimene cili cabwino kapena coipa. Adamu na Hava anapandukila Mulungu mwa kudya cipatso ca mtengo wodziŵitsa cabwino na coipa. Iwo anacita izi pofuna kutenga ulamulilowo. Mosiyana na Adamu na Hava, Yesu anadzicepetsa, ndipo anasiya nkhani ya kuika miyezo ya zinthu m’manja mwa Atate wake. Mulungu amationetsa na kutifotokozela zimene zili zabwino kupitila m’malamulo amene anaika m’Mau ake.—Maliko 10:19.

MAY 21-27

CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU | MALIKO 11-12

“Mkaziyo Anaponya Zambili Kuposa Ena Onse”

nwtsty mfundo zounikila pa Maliko 12:41, 42

moponyamo zopeleka: Zolemba zakale zaciyuda zimati mabokosi a zopeleka amenewa kapena kuti zoponyamo zopeleka, zinali kupangiwa monga citolilo kapena nyanga, mwacionekele na kam’boo kakang’ono pamwamba. Anthu anali kuponyamo zopeleka zawo. Liu lacigiriki limene aseŵenzetsa apa lipezekanso pa Yoh. 8:20, pamene anaimasulila kuti “malo a zopeleka.” Cioneka kuti mau amenewa atanthauza malo opezeka mkati mwa Bwalo la Akazi. (Onani mfundo younikila pa Mat. 27:6 na Gawo 15 m’Buku Lothandiza Pophunzila Mau A Mulungu.) Malinga na zolemba za Arabi, zoponyamo zopeleka zokwanila 13 zinaikiwa ku zipupa m’bwalo lonse. Anthu amakhulupilila kuti m’kacisi munalinso malo osungilamo zopeleka zonse zocoka m’zoponyelamo zopeleka.

timakobidi tiŵili tating’ono: Kapena kuti “maleputoni aŵili amene ni kuadirani.” Maleputoni ni mau oculukitsa liu lakuti le·ptonʹ m’cigiriki, kutanthauza kanthu kakang’ono komanso koyonda. Kaleputoni kanali kakoini kakang’ono ka kopa kapena ka citsulo kamene kanali kugwilitsidwa nchito mu Isiraeli. Maleputoni okwana 128 anali kupanga dinari imodzi. Liu la cigiriki lakuti ko·dranʹtes (lotengewa ku liu la Cilatini lakuti quadrans) limatanthauza ndalama zaciroma za kopa kapena za citsulo. Makuadirani okwana 64, anali kupanga dinari imodzi. Pa lembali, Maliko anaseŵenzetsa ndalama yaciroma pofotokoza mphamvu ya ndalama imene Ayuda anali kuseŵenzetsa.—Onani Gawo 18, m’Buku Lothandiza Pophunzila Mau a Mulungu.

Kufufuza Cuma ca Kuuzimu

nwtsty mfundo younikila pa Maliko 11:17

nyumba yopemphelelamo mitundu yonse: Pa anthu atatu olemba Mauthenga Abwino komanso amene anagwila mau apa Yes. 56:7, ni Maliko cabe amene analembanso mau akuti “mitundu yonse [anthu].” (Mat. 21:13; Luka 19:46) Kacisi wa ku Yerusalemu anali malo amene Aisiraeli na anthu acilendo oopa Mulungu anali kupemphelelamo na kulambililamo Yehova. (1 Maf. 8:41-43) Yesu anadzudzula Ayuda amene anali kucitila malonda m’kacisi, n’kuipanga phanga la acifwamba. Zocita zawo zinalepheletsa anthu a mitundu yonse kuyandikila Yehova m’nyumba yake yopemphelelamo, ndipo anaŵamanitsa mwayi womudziŵa.

MAY 28–JUNE 3

CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU | MALIKO 13-14

“Pewani Msampha wa Kuopa Anthu”

it-2 peji 619 pala. 6

Petulo

Petulo analoŵa m’bwalo lamkati kunyumba ya mkulu wa ansembe mothandiziwa na wophunzila wina, amene ayenela kuti anali kum’konkha kapena kum’pelekeza. (Yoh. 18:15, 16) Iye sanakhale cete n’kudzibisa pakona mu mdima, koma anapita kukaotha moto. Kuyaka kwa motowo kunapangitsa kuti ena amuzindikile kuti anali kuyenda na Yesu. Kakambidwe kake kacigalileya nakonso kanamugwilitsa. Ataona zimenezo, Petulo anakana Yesu katatu, ndipo pothela pake, anayamba kutembelela na kulumbila. Tambala atalila kaciŵili kumalo ena mu mzindawo, Yesu “anaceuka ndi kuyang’ana Petulo.” Ndiyeno, Petulo anatuluka panja, na kuyamba kulila mopwetekedwa mtima. (Mat. 26:69-75; Maliko 14:66-72; Luka 22:54-62; Yoh. 18:17, 18; onani pa mutu wakuti COCKCROWING; OATH.) Komabe, pemphelo limene Yesu anapemphelela Petulo linayankhiwa, ndipo cikhulupililo ca Petulo sicinatheletu.—Luka 22:31, 32.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani