LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • mwb18 December tsa. 2
  • Wozunza Akhristu Mwankhaza Akhala Mlaliki Wokangalika

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Wozunza Akhristu Mwankhaza Akhala Mlaliki Wokangalika
  • Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2018
  • Nkhani Zofanana
  • Yesu Asankha Saulo
    Maphunzilo Amene Tingatengemo m’Baibo
  • Paulendo Wa Ku Damasiko
    Buku Langa La Nkhani Za M’baibo
  • Davide na Sauli
    Maphunzilo Amene Tingatengemo m’Baibo
  • Sauli—mfumu Yoyamba Ya Isiraeli
    Buku Langa La Nkhani Za M’baibo
Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2018
mwb18 December tsa. 2
Saulo wagwa pamene kuwala kocokela kumwamba kwamuunika

CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | MACHITIDWE 9-11

Wozunza Akhristu Mwankhaza Akhala Mlaliki Wokangalika

9:15, 16, 20-22

Saulo sanazengeleze kucitapo kanthu pa zimene anaphunzila. N’cifukwa ciani Saulo anacitapo kanthu pamene ena sanatelo? Cifukwa anali kuopa Mulungu koposa anthu, ndiponso anayamikila kwambili cifundo cimene Khristu anamuonetsa. Ngati mumaphunzila Baibo koma simunabatizike, kodi mudzatengela citsanzo ca Saulo mwa kucitapo kanthu mwamsanga pa zimene mumaphunzila?

KODI MUDZIŴA?

Aroma anapatsa Ayuda mphamvu zoweluza okha milandu ya pakati pawo. Komabe, Khoti yalikulu ya Ayuda, komanso wansembe, anali na mphamvu pa Ayuda onse kulikonse kumene anali. Ndiye cifukwa cake iwo anapatsa cilolezo Saulo kuti akamange Ayuda amene anakhala Akhristu, ngakhale kumadela akutali monga ku Damasiko.

Mapu yoonetsa Damasiko na Yerusalemu
    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani