LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • mwbr19 April masa. 1-7
  • Malifalensi a Kabuku ka Umoyo na Utumiki Wathu

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Malifalensi a Kabuku ka Umoyo na Utumiki Wathu
  • Malifalensi a kabuku ka Umoyo na Utumiki Wathu—2019
  • Tumitu
  • APRIL 1-7
  • APRIL 8-14
  • APRIL 22-28
  • APRIL 29–MAY 5
Malifalensi a kabuku ka Umoyo na Utumiki Wathu—2019
mwbr19 April masa. 1-7

Malifalensi a Kabuku ka Umoyo na Utumiki Wathu

APRIL 1-7

CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | 1 AKORINTO 7-9

“Umbeta ni Mphatso”

w11 1/15 17-18 ¶3

Muzigwilitsa Nchito Mwanzelu Nthawi Imene Simuli pa Banja

3 Nthawi zambili munthu amene sali pa banja amakhala ndi nthawi komanso ufulu wocita zambili kusiyana ndi amene ali pa banja. (1 Akor. 7:32-35) Izi zimamupatsa mwayi wowonjezela utumiki wake, wofutukula mtima wake kuti akonde anthu ambili komanso woti ayandikile Yehova. Cifukwa ca zimenezi, Akhristu ambili azindikila kuti kusakhala pa banja kuli ndi ubwino wake ndipo asankha “kucita zimenezi” pa moyo wawo wonse kapena kwa kanthawi. Pali ena amene poyamba sanasankhe kuti asakhale pa banja koma zinthu zitasintha anaganizila mofatsa za moyo wawo komanso kupemphela ndipo aona kuti Yehova akhoza kuwathandiza kuti akhazikike mumtima mwawo. Iwo aona kuti akhoza kukhalabe osakwatila kapena osakwatiwa.—1 Akor. 7:37, 38.

w08 7/15 27 ¶1

Mfundo Zazikulu za M’makalata a ku Korinto

7:33, 34—Kodi “zinthu za dziko” zimene mwamuna wokwatila kapena mkazi wokwatiwa amada nazo nkhawa ndi ziti? Paulo akunena za zinthu zofunika pamoyo wa tsiku ndi tsiku zimene Akhristu okwatila afunika kuda nazo nkhawa. Zinthuzi ndi monga, cakudya, zovala ndiponso nyumba, koma sizikuphatikizapo zinthu zoipa za dzikoli, zimene Akhristu amapeweratu.—1 Yoh. 2:15-17.

w96 10/15 12-13 ¶14

Umbeta—Khomo la Nchito Yopanda Coceukitsa

14 Mkhristu mbeta amene amagwilitsila nchito umbeta wake kulondola zonulilapo zadyela sacita “bwino koposa” Akhristu okwatila. Iye apitiliza ndi umbeta, osati “cifukwa ca ufumu,” koma pa zifukwa zaumwini. (Mateyu 19:12) Mwamuna kapena mkazi wosakwatila ayenela ‘kudela nkhaŵa zinthu za Ambuye,’ kukhala wofunitsitsa ‘kupeza ciyanjo ca Ambuye,’ ndi “kutumikila Ambuye kosaleka popanda coceukitsa.” Zimenezi zikutanthauza kupeleka cisamalilo cosagaŵanika pa kutumikila Yehova ndi Khristu Yesu. Ndi kokha mwa kucita zimenezo pamene amuna ndi akazi acikristu osakwatila amacita “bwino koposa” Akhristu okwatila.

Kufufuza Cuma ca Kuuzimu

lvs 251

Mfundo za Kumapeto

Nthawi zina, Akhristu angasankhe kupatukana ngakhale kuti sipanacitike cigololo. (1 Akorinto 7:11) Zifukwa zina zimene Mkhristu angasankhile kupatukana ni izi.

• Kulephela mwadala kusamalila banja: Ngati mwamuna akana kupezela banja zinthu zofunikila, cakuti banja lake likusoŵa ndalama kapena cakudya.—1 Timoteyo 5:8.

• Ciwawa: Ciwawa cofika pamlingo woika thanzi kapena moyo wamnzake paciwopsezo.—Agalatiya 5:19-21.

• Kuika paciopsezo ubale wa munthu na Yehova: Ngati mwamuna kapena mkazi alepheletsa mnzake kutumikila Yehova.—Machitidwe 5:29.

w00 7/15 31 ¶2

Mukhoza Kudzisunga M’dziko Laciweleweleli

Motelo acinyamata sayenela kuthamangila mu ukwati pamene angoyamba kumva kudzuka kwa zikhumbo za kugonana. Ukwati umafuna kudzipeleka, ndipo kukwanilitsa udindo umenewo kumafuna kuti munthu akhale wofikapo. (Genesis 2:24) Ndi bwino kuyembekeza mpaka munthu ‘utapitilila pa unamwali wako,’ nthaŵi imene malingalilo akugonana amakhala amphamvu ndipo angacititse munthu kusaganiza bwino. (1 Akorinto 7:36) Ndipotu n’kupanda nzelu ndiponso n’kucimwa kwakukulu kuti munthu wamkulu amene akufuna kukwatila kapena kukwatiwa acite zaciwelewele pacifukwa cokha cakuti sakupeza munthu woti adzakwatilane naye!

APRIL 8-14

CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | 1 AKORINTO 10-13

“Yehova ni Wokhulupilika”

w17.02 29-30

Mafunso Ocokela Kwa Aŵelengi

Mtumwi Paulo analemba kuti Yehova “sadzalola kuti muyesedwe kufika pamene simungapilile.” (1 Akor. 10:13) Kodi izi zitanthauza kuti Yehova amadziŵilatu mayeselo amene tingakwanitse kuwapilila, ndiyeno n’kusankhapo mayeselo amene tidzakumana nawo?

▪ Ngati zimenezi zinali zoona, ganizilani mmene zikanakhudzila umoyo wathu. Mwacitsanzo, m’bale wina amene mwana wake anadzipha anafunsa kuti: ‘Kodi Yehova anadziŵilatu kuti ine na mkazi wanga tidzakwanitsa kupilila imfa ya mwana wathu? Kodi izi zinacitika cifukwa cakuti Mulungu anaona kuti tikhoza kupilila?’ Kodi pali cifukwa comveka cokhulupilila kuti Yehova amalamulila zocitika za pa umoyo wathu m’njila ya conco?

Kupendanso mawu a Paulo a pa 1 Akorinto 10:13, kwatifikitsa pa mfundo iyi: Palibe cifukwa ca m’Malemba cokhulupilila kuti Yehova amadziŵilatu mayeselo amene tingakwanitse kuwapilila, ndiyeno malinga na zimene waona, n’kusankha mayeselo amene tingakumane nawo. Tiyeni tikambilane zifukwa zinayi zimene zatifikitsa pa mfundo imeneyi.

Coyamba, Yehova anapatsa anthu ufulu wodzisankhila zocita. Iye amafuna kuti tisankhe mmene tifuna kukhalila pa umoyo wathu. (Deut. 30:19, 20; Yos. 24:15) Ngati tasankha njila yabwino, tingayang’ane kwa Yehova kuti atsogolele mayendedwe athu. (Miy. 16:9) Koma tikasankha njila yolakwika tidzakumana ndi mavuto. (Agal. 6:7) Ngati kuti Yehova amasankha mayeselo amene angatigwele, kodi si ndiye kuti akupondeleza ufulu wathu wosankha?

Caciŵili, Yehova satiteteza ku “nthawi yatsoka ndi zinthu zosayembekezeleka.” (Mlal. 9:11) Munthu angapezeke m’ngozi cabe cifukwa cakuti zangocitika mwa tsoka. Yesu anakamba za anthu 18 amene anafa pangozi pamene nsanja inawagwela, ndipo anaonetsa kuti Mulungu sindiye anacititsa imfa ya anthu amenewo. (Luka 13:1-5) Kodi n’canzelu kuganiza kuti Mulungu amakonzelatu amene adzapulumuka ndi amene adzafa pa zinthu zotigwela mwadzidzidzi?

Cacitatu, aliyense wa ise amaloŵetsedwamo m’nkhani ya kukhala wokhulupilika. Kumbukilani kuti Satana anakaikila kukhulupilika kwa atumiki onse a Yehova. Iye anati sitingakhale okhulupilika kwa Yehova tikakhala pa mayeselo. (Yobu 1:9-11; 2:4; Chiv. 12:10) Ngati Yehova angatiteteze kuti tisakumane ndi mayeselo ena cifukwa coona kuti sitingawapilile, kodi sizikanaonetsa kuti zimene Satana anakamba zakuti timatumikila Mulungu cifukwa ca dyela n’zoona?

Cacinayi, Yehova safunika kudziŵilatu ciliconse cimene cidzaticitikila. Mfundo yakuti Mulungu amasankhilatu mayeselo amene tidzakumana nawo ionetsa kuti afunika kudziŵa zonse zokhudza tsogolo lathu. Koma mfundo imeneyi si ya m’Malemba. N’zoona kuti Mulungu angadziŵiletu za kutsogolo. (Yes. 46:10) Koma Baibo ionetsa kuti iye amasankha zocitika za kutsogolo zimene afuna kudziŵilatu. (Gen. 18:20, 21; 22:12) Iye amakwanitsa kudziŵa zamtsogolo, koma amaganizilanso ufulu wathu wosankha. Kodi si zimene tingayembekezele kwa Mulungu amene amalemekeza ufulu wathu, komanso amene nthawi zonse amaonetsa makhalidwe ake mwacikondi?—Deut. 32:4; 2 Akor. 3:17.

Nanga tiyenela kuwamvetsa bwanji mau a Paulo akuti: “Mulungu sadzalola kuti muyesedwe kufika pamene simungapilile”? Apa Paulo anali kukamba zimene Yehova amacita pamene tikumana ndi mayeselo, osati tikalibe tikukumana nawo. Mawu a mtumwiyo amatitsimikizila kuti olo tikumane na mayeselo yabwanji, Yehova adzatithandiza ngati timudalila. (Sal. 55:22) Mawu otonthoza a Paulo ni ozikidwa pa mfundo ziŵili zofunika za coonadi.

Yoyamba, mayeselo amene timakumana nawo ‘amagwelanso anthu ena.’ Inde, mayeselo amene timakumana nawo ndi amenenso anthu ena amakumana nawo. Tikhoza kupilila mayeselo amenewa malinga ngati tidalila Mulungu. (1 Pet. 5:8, 9) Pokamba mawu a pa 1 Akorinto 10:13, Paulo anayelekezela ndi mayeselo amene Aisiraeli anakumana nawo m’cipululu. (1 Akor. 10:6-11) Pa mayeselo amenewo, palibe ciyeso cimodzi cimene cinali cacilendo kwa anthu kapena cimene Aisiraeli okhulupilika sakanatha kupilila. Paulo anacita kukamba kanayi kuti “ena mwa iwo” sanamvele. N’zacisoni kuti Aisiraeli ena anakodwa m’zilako-lako zoipa cifukwa colephela kudalila Mulungu.

Yaciŵili, “Mulungu ndi wokhulupilika.” Mbili ya mmene Mulungu anali kucitila zinthu ndi anthu ake ionetsa kuti iye amaonetsa cikondi cake cokhulupilika kwa “anthu amene amam’konda ndi kusunga malamulo ake.” (Deut. 7:9) Mbili imeneyi ionetsanso kuti Mulungu nthawi zonse amasunga malonjezo ake. (Yos. 23:14) Mwa kupenda mbili ya kukhulupilika kwake, anthu amene amam’konda ndi kumumvela angakhale ndi cidalilo cakuti iye adzasunga lonjezo lake lozikidwa pa mfundo ziŵili ngakhale akumane ndi mayeselo: (1) Iye sadzalola mayeselo aliwonse kufika pamene sitingakwanitse kuwapilila, ndipo (2) ‘adzapeleka njila yotipulumutsila.’

Kodi Yehova amapeleka bwanji njila yopulumukila kwa anthu amene amam’dalila panthawi ya mayeselo? N’zoona kuti angacotse mayeselowo ngati afuna. Koma kumbukilani Mau a Paulo akuti: “Iye [Yehova] adzapeleka njila yopulumukila kuti muthe kuwapilila.” Conco, nthawi zambili, iye ‘amapeleka njila yopulumukila’ mwa kutipatsa zimene tifunikila kuti tikwanitse kupilila mayeselowo. Onani njila zina za mmene Yehova angapelekele njila yopulumukila:

▪ Iye “amatitonthoza m’masautso athu onse.” (2 Akor. 1:3, 4) Yehova angatsitsimule maganizo ndi mtima wathu. Angacite zimenezi kupitila m’Mawu ake, mzimu wake woyela, ndi cakudya cauzimu cimene timalandila kwa kapolo wokhulupilika ndi wanzelu.—Mat. 24:45; Yoh. 14:16, Aroma. 15:4.

▪ Iye angatitsogolele pogwilitsila nchito mzimu woyela. (Yoh. 14:26) Tikakumana ndi mayeselo, mzimu ungatithandize kukumbukila nkhani za m’Baibo ndi mfundo zimene zingatithandize kusankha mwanzelu.

▪ Angagwilitsile nchito angelo ake kuti atithandize.—Aheb. 1:14.

▪ Angatithandize pogwilitsila nchito olambila anzathu. Mawu awo ndi zocita zawo ‘zingatithandize ndi kutilimbikitsa.’—Akol. 4:11.

Conco, kodi tingati mawu a Paulo a pa 1 Akorinto 10:13, atanthauza ciani? Yehova satisankhila mayeselo amene timakumana nawo. Koma tikakumana ndi mayeselo, tizikhala otsimikiza za izi: Ngati tili ndi cidalilo conse mwa Yehova, iye sadzalola kuti mayeselo athu afike poti sitingakwanitse kuwapilila. Nthawi zonse adzapeleka njila yopulumukila kuti tikwanitse kuwapilila. Imeneyi ni mfundo yolimbikitsa kwambili.

Kufufuza Cuma ca Kuuzimu

w04 4/1 29

Mafunso Ocokela kwa Oŵelenga

N’cifukwa ciani pa 1 Akorinto 10:8 amanena kuti Aisraeli amene anaphedwa tsiku limodzi cifukwa cocita dama anali 23,000 pamene pa Numeri 25:9 amati anali 24,000?

Pali zifukwa zingapo zimene zingacititse kuti pakhale kusiyana kwa manambala amene awachula m’mavesi aŵiliwa. Cifukwa cosavuta cingakhale cakuti ciŵelengelo ceni-ceni cinali pakati pa 23,000 ndi 24,000, zimene ngati munthu atalemba m’masauzande mokha angalembe 23,000 kapena 24,000.

Taonani cifukwa cinanso cimene cingakhale kuti n’cimene cinacititsa zimenezo. Mtumwi Paulo ananena zimene zinacitikila Aisraeli ku Sitimu monga citsanzo cowacenjeza Akhristu a ku mzinda wakale wa Korinto, umene unali wochuka ndi ciwelewele. Iye analemba kuti: “Tisacite dama monga ena a iwo anacita dama, nagwa tsiku limodzi zikwi makumi aŵili ndi zitatu.” Paulo anachula nambalayo kuti inali 23,000 pofuna kungopatulapo anthu amene Yehova anawapha cifukwa coti anacita dama.—1 Akorinto 10:8.

Koma mu Numeri caputala 25, amatiuza kuti “Israeli anaphatikana ndi Baala Peori, Mulungu anapsa mtima pa Israeli.” Ndiyeno Yehova analamula Mose kuti aphe “akulu onse a anthu.” Naye Mose anauza oweluza kuti acite zimene Yehova anamulamulazo. Kenako, pamene Pinehasi anacitapo kanthu mwamsanga kupha Mwiisrayeli amene anabweletsa mkazi wacimidyani mumsasa, “mlili unaletseka.” Nkhaniyo ikumaliza ndi mawu akuti: “Akufa nawo mlili ndiwo zikwi makumi aŵili ndi zinayi.”—Numeri 25:1-9.

Nambala imene aichula m’buku la Numeri mwacionekele inaphatikizapo “akulu onse a anthu” amene anaphedwa ndi oweluza ndiponso anthu amene anaphedwa mwacindunji ndi Yehova. Zingatheke kuti akulu a anthuwo amene anaphedwa ndi oweluza analipo okwana wani sauzande, zimene zinacititsa kuti nambalayo ikwane 24,000. Kaya akulu amenewa, kapena kuti atsogoleli, anacita nawo dama, mapwando, kapena kugwilizana ndi anthu amene anacita zimenezo, koma anali ndi mlandu ‘wophatikana ndi Baala Peori.’

Pankhani ya liwu lakuti “kuphatikana,” buku lina lofotokozela Baibulo linanena kuti liwuli lingatanthauze kuti “kudzigwilizanitsa ndi munthu wina.” Aisraeli anali anthu odzipatulila kwa Yehova, koma pamene “anaphatikana ndi Baala Peori,” anacita zinthu zosemphana ndi kudzipatulila kwawo kwa Mulungu. Patapita zaka pafupi-fupi 700, Yehova ananena za Aisraeli kudzela mwa mneneli Hoseya kuti: “Anadza kwa Baala Peori, nadzipatulila conyansaco, nasandulika onyansa, conga cija anacikonda.” (Hoseya 9:10) Anthu onse amene anacita zimenezo anayenelela kulangidwa ndi Mulungu. Motelo, Mose anakumbutsa ana a Israeli kuti: “Maso anu anapenya cocita Yehova cifukwa ca Baala Peori; pakuti amuna onse amene anatsata Baala Peori, Yehova Mulungu wanu anawawononga pakati panu.”—Deuteronomo 4:3.

w15 2/15 30

Mafunso Ocokela Kwa Aŵelengi

Kodi mlongo ayenela kuvala cakumutu pamene akucititsa phunzilo la Baibulo limodzi ndi mwamuna wofalitsa?

▪ Nkhani yakuti “Mafunso Ocokela kwa Owelenga” ya mu Nsanja ya Olonda ya July 15, 2002, inafotokoza kuti mlongo ayenela kuvala cakumutu ngati akucititsa phunzilo la Baibulo limodzi ndi mwamuna kaya ndi wobatizidwa kapena ayi. Komabe, pakhalako masinthidwe ena okhudza nkhani imeneyi.

Ngati mlongo wapita ndi m’bale wobatizidwa kukacititsa phunzilo la Baibulo, mlongoyo ayenela kuvala cakumutu. Akacita zimenezi, amaonetsa kuti akulemekeza makonzedwe a Yehova okhudza umutu mumpingo wacikhristu, cifukwa cakuti kuphunzitsa ndi udindo wa abale. (1 Akor. 11:5, 6, 10) Koma ngati afuna, angapemphe m’bale wobatizidwa kuti acititse phunzilo limenelo ngati m’baleyo ndi woyenelela.

Komabe, ngati mlongo wapita ndi mwamuna wosabatizidwa kukacititsa phunzilo la Baibulo lokhazikika, ndipo mwamunayo si mwamuna wake, iye safunikila kuvala cakumutu monga mmene Malemba amakambila. Ngakhale zili conco, alongo ena cikumbumtima cawo cingawalole kuvala cakumutu pazocitika ngati zimenezi.

APRIL 22-28

CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | 1 AKORINTO 14-16

“Mulungu Adzakhala ‘Zinthu Zonse kwa Aliyense’”

w98 7/1 21 ¶10

‘Imfa Idzathetsedwa’

10 “Cimalizilo” ndico cimalizilo ca Ulamulilo wa Khristu wa Zaka Cikwi, pamene Yesu modzicepetsa ndi mokhulupilika akukapeleka Ufumu kwa Mulungu ndi Atate wake. (Chivumbulutso 20:4) Cifuno ca Mulungu ca ‘kusonkhanitsa pamodzi zonse mwa Khristu’ cidzakhala citakwanilitsidwa. (Aefeso 1:9, 10) Komabe, coyamba Khristu adzaphwanya “ciweluzo conse, ndi ulamulilo wonse, ndi mphamvu yomwe” zotsutsana ndi cifuno ca Ucifumu wa Mulungu. Zimenezi zimaposa ciwonongeko ca pa Aramagedo. (Chivumbulutso 16:16; 19:11-21) Paulo anati: “[Khristu] ayenela kucita ufumu kufikila ataika adani onse pansi pa mapazi ake. Mdani wotsiliza amene adzathedwa ndiye imfa.” (1 Akorinto 15:25, 26) Inde, zotsalila zonse za ucimo wa Adamu ndi imfa zidzakhala zitacotsedwa. Conco cimene cidzakhala cofunika n’cakuti Mulungu adzasiya “manda” ali opanda kanthu mwa kuukitsamo akufawo.—Yohane 5:28.

kr 237 ¶21

Ufumu Ukwanilitsa Cifunilo ca Mulungu Padziko Lapansi

21 Nanga bwanji ponena za imfa imene kaŵili-kaŵili imabwela cifukwa ca ucimo umene umacitsa kuti tizidwala? Imfa ndi “mdani womalizila,” ndipo palibe munthu wopanda ungwilo amene angaipewe. (1 Akor. 15:26) Koma kodi imfa ndi mdani woopsa ngakhale kwa Yehova? Onani zimene Yesaya analosela ponena za Mulungu: “Iye adzameza imfa kwamuyaya ndipo Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, adzapukuta misozi pankhope zonse za anthu.” (Yes. 25:8) Taganizilani mmene zinthu zidzakhalila panthawi imene kudzakhala kulibe malilo, manda, kapena misozi ya cisoni. M’malo mwake anthu adzakhala ndi misozi ya cikondwelelo poona kuti Yehova akukwanilitsa lonjezo lake la kuukitsa anthu akufa. (Ŵelengani Yesaya 26:19) Pomalizila pake, mavuto onse obwela cifukwa ca imfa adzatha.

w12 9/15 12 ¶17

Mtendele Udzayamba mu Ulamulilo wa Zaka 1,000

17 Mawu osangalatsa kwambili ndi akuti ‘Mulungu adzakhala zinthu zonse kwa aliyense.’ Zimenezi zidzacitika kumapeto kwa Ulamulilo wa Zaka 1,000. Koma kodi mawu amenewa amatanthauza ciani? Taganizilani mmene zinalili Adamu ndi Hava ali angwilo mu Edeni. Iwo anali m’banja la Yehova lamtendele ndiponso logwilizana. Yehova monga Wolamulila wa Cilengedwe Conse anali kulamulila mwacindunji angelo ndiponso anthu. Iwo anali kulankhula naye komanso kumulambila. Mulungu anali kuwadalitsa ndipo iye anali “zinthu zonse kwa aliyense.”

Kufufuza Cuma ca Kuuzimu

w12 9/1 9, bokosi

Kodi Mtumwi Paulo Analetsa Akazi Kulankhula?

Mtumwi Paulo analemba kuti: “Akazi akhale cete m’mipingo.” (1 Akorinto 14:34) Kodi iye anatanthauza ciani ponena mawu amenewa? Kodi anali kuwadelela akazi? Ayi, cifukwatu iye anena kuti akazi amaphunzitsa zinthu zothandiza. (2 Timoteyo 1:5; Tito 2:3-5) M’kalata yake yopita kwa Akorinto, Paulo sanangolangiza akazi okha koma analangizanso amuna, omwe anali ndi mphatso yolankhula malilime komanso yonenela, kuti ‘azikhala cete’ munthu wina akamalankhula. (1 Akorinto 14:26-30, 33) Ziyenela kuti akazi ena anali kusangalala kwambili ndi zimene anali kuphunzila mumpingo moti munthu wina akamalankhula anali kumudula mawu n’kuyamba kumufunsa mafunso. Izi zinali zofala pa nthawiyo. Conco kuti pasakhale cisokonezo, Paulo anawauza kuti ‘azikafunsa amuna awo kunyumba.’—1 Akorinto 14:35.

it-1 1197-1198

Kusawonongeka

Pokhala ogwilizana na Yesu poukitsidwa mofanana na iye, olamulila anzake nawonso amaukitsidwa kuti akhale na moyo wosafa komanso wosawonongeka. Iwo akatumikila mokhulupilika, na kumwalila m’matupi aumunthu amene amawonongeka, amaukitsidwa na matupi auzimu amene sangawonongeke, monga mmene Paulo anakambila momveka bwino pa 1 Akorinto 15:42-54. Mawu akuti moyo wosakhoza kufa mwacionekele atanthauza mtundu wa moyo umene iwo adzakhala nawo. Udzakhala moyo wopanda mapeto, umene sungafe. Koma mawu akuti wosakhoza kuwonongeka mwacionekele akamba za mtundu wa thupi lauzimu limene Mulungu adzawapatsa. Lidzakhala thupi lakuti silingawole kapena kuti kuvunda. Conco, zioneka kuti Mulungu adzawapatsa mphamvu yokhala na moyo pa iwo okha, popanda kudalila mphamvu inayake ya kunja kwa thupi lawo, monga mmene zilili na zolengedwa zake zina, kaya zathupi lanyama kapena zauzimu. Umenewu ni umboni wamphamvu woonetsa kuti Mulungu amawakhulupilila. Komabe, kukhala na mphamvu zotelo sikutanthauza kuti sazidalilanso Mulungu. Iwo mofanana na Mutu wawo Yesu Khristu, amapitiliza kucita cifunilo ca Atate wawo na kugonjela zitsogozo zake.—1 Akorinto 15:23-28.

APRIL 29–MAY 5

CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | 2 AKORINTO 1-3

“Yehova ni ‘Mulungu Amene Amatitonthoza M’njila Iliyonse’”

w17.07 13 ¶4

“Lilani Ndi Anthu Amene Akulila”

4 Atate wathu wacifundo cacikulu anavutikapo na cisoni cifukwa ca imfa ya okondedwa ake monga Abulahamu, Isaki, Yakobo, Mose, ndi Mfumu Davide. (Num. 12:6-8; Mat. 22:31, 32; Mac. 13:22) Mawu a Mulungu amakamba kuti Yehova amacita kulaka-laka nthawi pamene adzaukitsa akufa. (Yobu 14:14, 15) Anthuwo akadzaukitsidwa, adzakhala osangalala ndi athanzi. Komanso, kumbukilani kuti Mwana wokondeka wa Mulungu, amene anali kusangalala naye kwambili, anafa imfa yoŵaŵa. (Miy. 8:22, 30) Sitingakwanitse kufotokoza mmene Yehova cinamuwaŵila panthawiyo.—Yoh. 5:20; 10:17.

w17.07 15 ¶14

“Lilani Ndi Anthu Amene Akulila”

14 M’pomveka kuti nthawi zina munthu amasoŵa cokamba kwa munthu amene ali na cisoni cacikulu. Ngakhale n’conco, Baibo imakamba kuti “lilime la anthu anzelu limacilitsa.” (Miy. 12:18) Pofuna kutonthoza ena, ambili apeza mfundo zolimbikitsa m’kabuku kakuti, Pamene Munthu Amene Mumakonda Amwalira. Komabe, nthawi zambili cimene cimakhala cothandiza kwambili ndi ‘kulila ndi anthu amene akulila.’ (Aroma 12:15) Gaby, amene mwamuna wake anamwalila, anati: “Kulila n’kumene kumanitonthoza. N’cifukwa cake nimalimbikitsidwa ngati anzanga akulila nane. Panthawiyi, nimatonthozedwa poona kuti anzanga nawonso ali na cisoni.”

Kufufuza Cuma ca Kuuzimu

w16.04 32

Mafunso Ocokela kwa Oŵelenga

Kodi odzozedwa amalandila bwanji “cikole” nanga amadindidwa bwanji “cidindo”?—2 Akor. 1:21, 22.

▪ Cikole: Buku lina limanena kuti mawu acigiriki amene anawamasulia kuti “cikole” pa 2 Akorinto 1:22, “ankawagwilitsa nchito pa zinthu zokhudza malamulo komanso malonda.” Mawuwa amatanthauza “ndalama zocepa zimene munthu amapeleka coyamba, pogula cinthu. Ndalamazi zimatsimikizila kuti mwagwilizanadi kuti mudzagulitsana cinthuco ndipo malipilo onse adzapelekedwa.” Mkhristu akadzozedwa amakhala kuti walandila cikole, koma malipilo onse amene adzalandile afotokozedwa pa 2 Akorinto 5:1-5. Odzozedwa adzapita kumwamba ndipo adzakhala ndi moyo wosafa.—1 Akor.15:48-54.

M’Cigiriki ca masiku ano, mawu ofanana ndi akuti cikole amawagwilitsanso nchito ponena za mphete ya ukwati. Zimenezi n’zomveka tikaganizila mfundo yoti odzozedwa adzakhala ngati mkazi wa Khristu.—2 Akor. 11:2; Chiv. 21:2, 9.

▪ Cidindo: Kale cidindo anali kucigwilitsa nchito ngati sigineca posonyeza mwini wa cinthu, potsimikizila kuti cinthuco n’ceni-ceni komanso posonyeza kuti anthu anagwilizana zinazake. Tingati Akhristu odzozedwa ‘anadindidwa’ ndi mzimu woyela posonyeza kuti ndi a Mulungu. (Aef. 1:13, 14) Komabe kutsimikizila kweni-kweni kumacitika Mkhristu wodzozedwa akatsala pang’ono kumwalila ali wokhulupilika kapena kudzacitika cisautso cacikulu citatsala pang’ono kuyamba.—Aef. 4:30; Chiv. 7:2-4.

w10 8/1 23

Kodi Mukudziŵa?

Kodi Paulo pochula mawu akuti “cionetselo ca kupambana” ankanena za ciani?

▪ Paulo analemba kuti: “Mulungu . . . amatitsogolela poguba pamodzi ndi Khristu pa cionetselo ca kupambana. Kudzela mwa ife, Mulungu akupangitsa fungo labwino la kum’dziŵa iye kumveka ponse-ponse! Pakuti pamaso pa Mulungu ndife fungo la Khristu lonunkhila bwino kwa anthu amene akupulumuka ndi amene akuwonongeka. Kwa amene akuwonongekawo ndife fungo locokela ku imfa kupita ku imfa, kwa amene akupulumuka ndife fungo locokela ku moyo kupita ku moyo.”—2 Akorinto 2:14-16.

Pamenepa, mtumwi Paulo anali kunena za cikondwelelo cimene Aroma anali kucita pofuna kulemekeza mkulu wa asilikali amene wagonjetsa adani a Boma. Iwo anali kucita cikondwelelo cimeneci akuyenda mumsewu. Pa zocitika zimenezi, Aromawo anali kuonetsa anthu zimene afunkha komanso akaidi ogwidwa kunkhondo. Iwo anali kutenga ng’ombe n’kupita nazo kumalo opelekela nsembe, kwinaku akukondwela ndi kutamanda mkulu wa asilikaliyo ndi gulu lake lankhondo. Pa mapeto pake anali kupeleka nsembe ng’ombe zija ndipo n’kutheka kuti ambili mwa akaidiwo anali kuwapha.

Buku lina limanena kuti pamene Paulo ananena za “fungo la Khristu lonunkhila bwino” lotanthauza moyo kwa anthu ena komanso imfa kwa ena, “ayenela kuti anali kuyelekezela ndi zimene Aroma anali kucita pa zionetselo zawo za kupambana. Pa zionetselozi anali kufukiza nsembe zonunkhila, kwinaku akuguba mumsewu.” Bukulo limanenanso kuti: “Kwa Aroma, fungo limenelo linali kutanthauza kuti apambana, pamene kwa akaidi ogwidwa kunkhondowo linali kungowakumbutsa za clilango ca imfa cimene anali kuyembekezela kulandila.”—The International Standard Bible Encyclopedia.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani