May 20-26
2 AKORINTO 11-13
Nyimbo 3 na Pemphelo
Mawu Oyamba (3 min. olo kucepelapo)
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
“‘Munga M’thupi’ la Paulo”: (10 min.)
2 Akor. 12:7—Paulo analimbana na vuto limene linali ngati munga wopweteka (w08 6/15 3-4)
2 Akor. 12:8, 9—Yehova anasankha kusayankha pembedzelo la Paulo lakuti amucotsele vutolo (w06 12/15 24 ¶17-18)
2 Akor. 12:10—Paulo anakwanilitsa utumiki wake mwa kudalila mzimu woyela wa Mulungu (w18.01 9 ¶8-9)
Kufufuza Cuma ca Kuuzimu: (8 min.)
2 Akor. 12:2-4—Kodi “kumwamba kwacitatu” komanso “paradaiso” ziyenela kuti zitanthauza ciani? (w18.12 8 ¶10-12)
2 Akor. 13:12—Kodi mawu akuti “kupsompsonana kwaubale” amanena za ciani? (it-2 177)
Kodi imwe pacanu, kuŵelenga Baibo kwa wiki ino kwakuphunzitsani ciani za Yehova?
Ni cuma ca kuuzimu cina citi cimene mwapeza pa kuŵelenga Baibo kwa wiki ino?
Kuŵelenga Baibo: (4 min. olo kucepelapo) 2 Akor. 11:1-15 (th phunzilo 5)
CITANI KHAMA PA ULALIKI
Vidiyo ya Ulendo Wobwelelako Woyamba: (5 min.) Tambitsani na kukambilana vidiyoyi.
Ulendo Wobwelelako Woyamba: (3 min. olo kucepelapo ) Seŵenzetsani makambilano acitsanzo. (th phunzilo 2)
Ulendo Wobwelelako Woyamba: (4 min. olo kucepelapo) Yambani na makambilano acitsanzo, ndiyeno gaŵilani buku la Zimene Baibulo Ingatiphunzitse. (th phunzilo 4)
UMOYO WATHU WACIKHRISTU
“Mungapambane Ngakhale Kuti Muli na ‘Munga M’thupi’!”: (15 min.) Kukambilana. Tambitsani vidiyo yakuti “Maso a anthu akhungu adzatseguka”. Dziŵitsani omvetsela kuti mabuku a akhungu kapena kuti a anthu osaona apezeka mu zitundu 47, m’kalembedwe ka akhungu komanso m’mitundu ina. Ofalitsa afunika kuuza mtumiki wa mabuku kuti aitanitse mabukuwo. Limbikitsani omvetsela onse kuti azikhala chelu komanso okonzeka kuthandiza aliyense amene ni wakhungu mumpingo kapena m’gawo.
Phunzilo la Baibo la Mpingo: (30 min.) jy mutu 67
Kubwelelamo na Kuchulako za Wiki Yotsatila (3 min.)
Nyimbo 78 na Pemphelo