CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | 2 AKORINTO 11-13
“Munga M’thupi” la Paulo
Nthawi zambili, Baibo imaseŵenzetsa liwu lakuti minga mlingalilo lophiphilitsa. Minga zingatanthauze anthu ovutitsa ena kapena amene amavulaza ena. Zingatanthauzenso zinthu zimene zingabweletse mavuto. (Num. 33:55; Miy. 22:5; Ezek. 28:24) Paulo, polemba za “munga m’thupi,” mwina anali kutanthauza atumwi onyenga, kapenanso anthu ena amene anali kukayikila utumwi wake na nchito zake. Kodi malemba ali munsimu aonetsa zinthu zina ziti zimene mwina zinali “munga m’thupi” kwa Paulo?
Nanga imwe, ‘munga wanu m’thupi’ n’ciani?
Ndipo mungadalile motani pa Yehova kuti akuthandizeni kuupilila?