LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • mwb19 November tsa. 3
  • Pewani Kutengela Maganizo a Dziko Pokonzekela Cikwati

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Pewani Kutengela Maganizo a Dziko Pokonzekela Cikwati
  • Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2019
Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2019
mwb19 November tsa. 3
Pikica ya banja pa tsiku la cikwati

UMOYO WATHU WACIKHRISTU

Pewani Kutengela Maganizo a Dziko Pokonzekela Cikwati

M’bale na mlongo amene ali pa citomelo, amafunika kupanga zosankha zambili pokonzekela cikwati cawo. Iwo angafunitsitse kucita cikwati capamwamba monga mmene vikwati vina vimacitikila m’dela lawo. Mabwenzi komanso acibululu, angakhale na maganizo awo pa zinthu zimene ziyenela kuloŵetsedwamo pokonzekela cikwati. Kodi ni mfundo ziti za m’Baibo zimene zingathandize oloŵa m’banjawo kukonzekela tsiku lapadela limeneli, m’njila yakuti asadzakhale na cikumbumtima covutitsidwa kapena kudziimba mlandu pambuyo pake?

TAMBITSANI VIDIYO YAKUTI MAUKWATI AMENE AMALEMEKEZA YEHOVA, NDIYENO YANKHANI MAFUNSO OTSATILAWA:

  • Kodi mfundo za m’Baibo pa Malemba otsatilawa zinathandiza bwanji Nick na Juliana?

    • 1 Akor. 10:31

    • 1 Yoh. 2:15, 16

    • Agal. 5:19-21

    • 1 Tim. 2:9

  • N’cifukwa ciani mwamuna na mkazi amene afuna kucita cikwati ayenela kusankha m’bale wokhwima mwauzimu kuti akhale “woyang’anila phwando”?—Yoh. 2:9, 10.

  • N’cifukwa ciani Nick na Juliana anasankha kuti cikwati cawo cicitike mwanjila imeneyo?

  • N’ndani ali na udindo wopanga zosankha zokhudza phwando la cikwati komanso kocitila?—w06 10/15 25 ¶10

Mapikica: Zocitika za mu vidiyo yakuti ‘Maukwati Amene Amalemekeza Yehova.’ Nick na Juliana akukonzekela za cikwati cawo, ndipo afunika kupanga zosankha zambili. 1. Iwo akupemphela payekha-payekha. 2. Tabuleti na mapepa oonetsa zimene anafufuza. 3. Iwo akukambilana na banja zimene adzacita pa tsiku la cikwati cawo. 4. Iwo pamodzi na acibanja komanso anzawo akukonza makhadi oitanila anthu ku cikwati.
    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani