LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • mwbr19 December
  • Malifalensi a Kabuku ka Umoyo na Utumiki

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Malifalensi a Kabuku ka Umoyo na Utumiki
  • Malifalensi a kabuku ka Umoyo na Utumiki Wathu—2019
  • Tumitu
  • DECEMBER 2-8
  • DECEMBER 9-15
  • DECEMBER 16-22
  • DECEMBER 23-29
  • DECEMBER 30–JANUARY 5
Malifalensi a kabuku ka Umoyo na Utumiki Wathu—2019
mwbr19 December

Malifalensi a Kabuku ka Umoyo na Utumiki

DECEMBER 2-8

CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | CHIVUMBULUTSO 7-9

“Khamu Lalikulu Losaŵelengeka Likudalitsidwa na Yehova”

it-1 997 ¶1

Khamu Lalikulu

Funso n’lakuti: Ngati a “khamu lalikulu” ni anthu amene adzapulumuka na kukhala padziko lapansi, n’cifukwa ciani akunenedwa kuti ‘adzaimilila pamaso pa mpando wacifumu [wa Mulungu] ndi pamaso pa Mwanawankhosa’? (Chiv. 7:9) Mu Baibo, mawu akuti ‘kuimilila’ pamaso pa winawake nthawi zina amatanthauza kuti munthuyo kapena gululo ni loyanjidwa. (Sal. 1:5; 5:5; Miy. 22:29, AT, Luka 1:19) Ndipo caputa 6 ya buku la Chivumbulutso imafotokoza kuti, “mafumu a dziko lapansi, nduna, akuluakulu a asilikali, olemela, amphamvu, kapolo aliyense ndi mfulu aliyense” anabisala kuti ‘asaonekele kwa Iye amene wakhala pampando wacifumu, ndiponso kuti abisike ku mkwiyo wa Mwanawankhosa, cifukwa tsiku lalikulu la mkwiyo wawo lafika, ndipo ndani angaimilile pamaso pawo?’ (Chiv. 6:15-17; yelekezelani na Luka 21:36.) Conco n’zoonekelatu kuti “khamu lalikulu” ni anthu amene adzapulumuka pa nthawi ya mkwiyo imeneyo, amenenso adzatha ‘kuimilila’ cifukwa coyanjidwa na Mulungu komanso Mwanawankhosa.

it-2 1127 ¶4

Cisautso

Patapita zaka pafupi-fupi 30 kucokela pamene mzinda wa Yerusalemu unawonongedwa, mtumwi Yohane anaona m’masomphenya khamu lalikulu la anthu ocokela m’mitundu yonse, zinenelo, ndi anthu. Kenako anauzidwa kuti: “Amenewa ndi amene atuluka m’cisautso cacikulu.” (Chiv. 7:13, 14) ‘Kutuluka m’cisautso cacikulu,’ kutanthauza kuti iwo adzapulumuka cisautso cimeneco. Izi zikuonekela m’mawu ofanana nawo opezeka pa Machitidwe 7:9, 10, akuti: “Mulungu anali naye [Yosefe], ndipo anamulanditsa m’masautso ake onse.” Mawu akuti Mulungu analanditsa Yosefe ku masautso ake onse satanthauza kuti anangom’thandiza kupilila cabe mavutowo ayi. Atanthauzanso kuti anamupulumutsa ku mavutowo.

it-1 996-997

Khamu Lalikulu

Kodi Iwo Ndani? Cimene cingatithandize kudziŵa kuti a “khamu lalikulu” n’ndani ni kupenda mawu ofotokoza za khamuli opezeka mu Chivumbulutso caputa 7, na m’macaputa ena. Chivumbulutso 7:15-17 imakamba kuti Mulungu “adzatambasulila hema wake pamwamba pawo,” komanso kuti adzawatsogolela ku “akasupe a madzi a moyo,” ndiponso kuti Mulungu adzapukuta “misozi yonse m’maso mwawo.” Mu Chivumbulutso 21:2-4 timapeza mawu ofanananso akuti: “Cihema ca Mulungu cili pakati pa anthu,” iye “adzapukuta misozi yonse m’maso mwawo, ndipo imfa sidzakhalaponso.” Masomphenya a m’mavesi amenewa sakamba za anthu akumwamba, kumene “Yerusalemu Watsopano, ukutsika.” Koma akamba za anthu a pa dziko lapansi.

Kufufuza Cuma ca Kuuzimu

re 115 ¶4

Kudinda Cidindo Isiraeli wa Mulungu

Mwacionekele, angelo anayi amenewa amaimila magulu anayi a angelo, amene Yehova akuwaseŵenzetsa kugwila mphepo za ciweluzo cake kufikila pa nthawi yoikika. Koma angelowo akadzatailila pa nthawi imodzi mphepo za mkwiyo wa Mulungu zimenezo, kuti zikawombe kucokela kumpoto, kum’mwela, kum’maŵa na kumadzulo, padzakhala kusakaza kwa dzaoneni. Ciwonongeko cake cidzafananako na cija pamene Yehova anagwilitsila nchito mphepo zinayi kubalalitsa mtundu wa Aelamu na kuwawononga onse kowathelatu. Koma ici cidzacitika pamlingo waukulu koopsa. (Yeremiya 49:36-38) Cidzakhala cimphepo cowononga kuposa “mphepo yamkuntho” imene Yehova anawononga nayo mtundu wa Amoni. (Amosi 1:13-15) Palibe mbali iliyonse ya gulu la Satana lapadziko lapansili imene idzapulumuka pa tsiku la mkwiyo wa Yehova. Yehova adzaonetsa kuti ndiye woyenela kulamulila, ndipo palibenso amene adzatsutse mpaka muyaya.—Salimo 83:15, 18; Yesaya 29:5, 6.

it-1 12

Abadoni

Kodi Abadoni mngelo wa phompho n’ndani?

Pa Chivumbulutso 9:11, mawu akuti “Abadoni” ni dzina la “mngelo wa phompho.” Dzina lofanana nalo la Cigiriki ni lakuti “Apoliyoni,” kutanthauza “Wowononga.” M’zaka za m’ma 1800, anthu ena anayesa kufotokoza kuti lemba limeneli ni ulosi, ndipo “Abadoni” aimila anthu monga Mfumu Vespasian, Muhammad, ngakhalenso Napoleon. Anafotokozanso kuti mngelo ameneyu ni “wa Satana.” Koma onani kuti lemba la Chivumbulutso 20:1-3, limaonetsa kuti mngelo wokhala na ‘kiyi ya ku phompho’ ameneyu amaimilako Mulungu, ndipo adzamanga Satana na kum’ponya ku phompho. Conco, sangakhale mngelo wa Satana. Pothilila ndemenga pa lemba la Chivumbulutso 9:11, Buku lochedwa Interpreter’s Bible, limati: “Abadoni ni mngelo wa Mulungu osati wa Satana. Iye amagwila nchito yake yowononga molamulidwa na Mulungu.”

Malemba a Ciheberi amene takambilana, aonetsa kuti liwu lakuti ʼavad·dohn,ʹ limafanananso na Sheol (Manda) na imfa. Pa Chivumbulutso 1:18, Yesu Khristu anati: “Ndili ndi moyo kwamuyaya, ndipo ndili ndi makiyi a imfa ndi a Manda.” Ndipo lemba la Luka 8:31 limaonetsa kuti iye ali na ulamulilo pa phompho. Komanso mfundo yakuti Yesu ali na mphamvu zowononga kuphatikizapo kuwononga Satana, imaonekela bwino pa Aheberi 2:14, pamene pamakamba kuti Yesu anakhala wamagazi na mnofu kuti “kudzela mu imfa yake, . . . awononge Mdyelekezi, amene ali ndi njila yobweletsela imfa.” Pa Chivumbulutso 19:11-16, iye akufotokozedwa momveka bwino kuti ndiye anasankhidwa na Mulungu monga Wowononga kapena kuti Wakupha.

DECEMBER 9-15

CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | CHIVUMBULUTSO 10-12

“Mboni Ziŵili Zinaphedwa, Kenako Zinakhalanso na Moyo”

w14 11/15 30

Mafunso Ocokela kwa Aŵelengi

Kodi mboni ziŵili zochulidwa pa Chivumbulutso caputa 11 ndani?

Lemba la Chivumbulutso 11:3 limanena za mboni ziŵili zimene zinali kudzalosela kwa masiku 1,260. Ndiyeno nkhaniyo imati, cilombo “cidzazigonjetsa ndi kuzipha.” Koma pambuyo pa “masiku atatu ndi hafu,” mboni ziŵili zimenezi zidzaukitsidwa. Ndipo anthu onse oona adzadabwa kwambili.—Chiv. 11:7, 11.

Kodi mboni ziŵilizi ndani? Nkhani yonse ya m’caputa imeneyi itithandiza kudziŵa mboni zimenezi. Coyamba, tikuuzidwa kuti mboni zimenezi “zikuimilidwa ndi mitengo iŵili ya maolivi, ndi zoikapo nyale ziŵili.” (Chiv. 11:4) Izi zitikumbutsa zoikapo nyale na mitengo iŵili ya maolivi, yochulidwa mu ulosi wa Zekariya. Mitengo ya maolivi imeneyo inaimila “odzozedwa aŵili,” Bwanamkubwa Zerubabele na Mkulu wa Ansembe Yoswa, amene ‘anaimilila kumbali iyi na mbali inayi ya Ambuye wa dziko lonse lapansi.’ (Zek. 4:1-3, 14) Caciŵili, mboni ziŵilizi akuti zikucita zizindikilo zofanana na zimene Mose na Eliya anacita.—Yelekezelani Chivumbulutso 11:5, 6 na Numeri 16:1-7, 28-35 komanso 1 Mafumu 17:1; 18:41-45.

Kodi cofanana pa Malemba amenewa n’ciani? Lemba lililonse limachula za odzozedwa a Mulungu, amene anali kutsogolela pa nthawi zovuta. Conco, pa kukwanilitsidwa kwa Chivumbulutso caputa 11, abale odzozedwa amene anali kutsogolela pamene Ufumu wa Mulungu unakhazikitsidwa kumwamba mu 1914, analalikila kwa zaka zitatu na hafu atavala “ziguduli.”

Atatsiliza kulalikila m’ziguduli, odzozedwa amenewa anapedwa mophiphilitsila, pamene anaponyedwa m’ndende kwa kanthawi, koimilidwa na masiku atatu na hafu. Kwa adani a anthu a Mulungu, nchito ya mboni zimenezo inakhala ngati yafa, zimene zinakondweletsa kwambili adani awo.—Chiv. 11:8-10.

Koma pokwanilitsa ulosi umenewu, kumapeto kwa masiku atatu na hafu, mboni ziŵilizo zinaukitsidwa. Odzozedwa amenewa sanangomasulidwa m’ndende cabe. Amene anakhalabe okhulupilika analandilanso udindo wapadela wocokela kwa Mulungu kupyolela mwa Mbuye wawo Yesu Khristu. Mu 1919, iwo pamodzi na odzozedwa ena anaikidwa kukhala “kapolo wokhulupilika ndi wanzelu,” kuti asamalile zosoŵa za kuuzimu za anthu a Mulungu m’masiku otsiliza.—Mat. 24:45-47; Chiv. 11:11, 12.

N’zocititsa cidwi kuti Chivumbulutso 11:1, 2 imagwilizanitsa zocitika zimenezi na nthawi pamene kacisi wa kuuzimu anali kudzayezedwa, kapena kupimidwa. Mofananamo, Malaki caputa 3 imachula za kuyendela kacisi wa kuuzimu, na kumuyeletsa pambuyo pake. (Mal. 3:1-4) Kodi nchito yoyendela kacisi na kumuyeletsa imeneyi inatenga utali wotani? Inayamba mu 1914, mpaka kuciyambi kwa 1919. Nthawi imeneyi imaphatikizapo masiku 1,260 (kapena miyezi 42), komanso masiku atatu na hafu ophiphilitsila ochulidwa pa Chivumbulutso caputa 11.

Ndife okondwa cotani nanga, kuti Yehova analinganiza nchito yoyenga mwauzimu imeneyo, kuti ayeletse anthu apadela kuti acite nchito zabwino! (Tito 2:14) Ndiponso, timayamikila citsanzo ca Akhristu odzozedwa okhulupilika, amene anatsogolela panthawi yovuta imeneyo, na kutumikila monga mboni ziŵili zophiphilitsila.

Kufufuza Cuma ca Kuuzimu

it-2 880-881

Mpukutu

Tanthauzo Lophiphilitsila. M’malo angapo m’Baibo liwu lakuti “mpukutu” lili na matanthauzo ophiphilitsila. Ezekieli na Zekariya onse anaona mpukutu wolembedwa mbali zonse ziŵili. Popeza kuti nthawi zambili mipukutu inali kulembedwa mbali imodzi, kulembedwa mbali zonse ziŵili kuyenela kuti kunaonetsa mphamvu ya uthenga waciweluzo wolembedwamo, ukulu wake, komanso kuwopsa kwake. (Ezek. 2:9–3:3; Zek. 5:1-4) M’masomphenya a Chivumbulutso, munthu wokhala pampando wacifumu anali na mpukutu m’dzanja lake lamanja womatidwa na zidindo 7, n’colinga cakuti aliyense asadziŵe zimene zinalembedwamo kufikila pamene Mwanawankhosa wa Mulungu adzazimatule. (Chiv. 5:1, 12; 6:1, 12-14) Pambuyo pake, m’masomphenyawo, Yohane anapatsidwa mpukutu wina ndipo analamulidwa kuti audye. Yohane anakamba kuti mpukutuwo unali wonzuna m’kamwa mwake koma m’mimba unali woŵaŵa. Popeza mpukutuwo unali wofunyulula ndiponso wosamatidwa, uthenga wake unali wosabisa. Kunali ‘konzuna’ kwa Yohane kumvetsa uthenga wa mpukutuwo, koma unali na ulosi woŵaŵa umene anafunika kuti anenele. (Chiv. 10:1-11) Zinalinso cimodzi-modzi kwa Ezekieli, amene anapatsidwa m’masomphenya mpukutu wokhala na “nyimbo zoimba polila, mawu odandaula ndi mawu olila.”—Ezek. 2:10.

it-2 187 ¶7-9

Zoŵaŵa za Pobeleka

M’masomphenya a mtumwi Yohane m’buku la Chivumbulutso, iye anaona mkazi wa kumwamba akulila “pomva ululu cifukwa ca zoŵaŵa za pobeleka.” Mwana wobadwayo anali “wamwamuna, mnyamata amene adzakusa mitundu yonse ndi ndodo yacitsulo.” Ngakhale kuti cinjoka cinafunitsitsa kuti cidye mwanayo, “anatengedwa msangamsanga n’kupititsidwa kwa Mulungu ndi kumpando wake wacifumu.” (Chiv. 12:1, 2, 4-6) Kutengedwa mwamsanga kwa mwanayo na Mulungu, kunaonetsa kuti Mulungu anavomela kuti mwanayo ni wake. Cinali cikhalidwe m’nthawi yakale kupeleka mwana amene wabadwa kwa atate ake kuti amuvomele. Conco, “mkazi” ameneyu ni mkazi wa Mulungu, kapena kuti ‘Yerusalemu Wakumiyamba,’ “mayi” wa Khristu na abale ake akuuzimu.—Agal. 4:26; Aheb. 2:11, 12, 17.

Mkazi wa Mulungu wakumwamba ni wangwilo, ndipo anabeleka mwana popanda zoŵaŵa zeni-zeni za pobeleka. Conco, zoŵaŵa za pobeleka zingophiphilitsila kuti ‘mkaziyo’ anazindikila kuti wangotsala pangono kubeleka.—Chiv. 12:2.

Nanga “mwana wamwamuna” ameneyu ndani? Iye anali ‘kudzakusa mitundu yonse ndi ndodo yacitsulo.’ Izi n’zimene zinakambidwilatu pa Salimo 2:6-9, ponena za Mfumu ya Mulungu Yaumesiya. Koma Yohane anaona masomphenya amenewa patapita nthawi yaitali kucokela pamene Khristu anabadwa padziko lapansi, kuphedwa na kuukitsidwa. Cotelo, masomphenyawa aoneka anali kukamba za kubadwa kwa Ufumu Wamesiya m’manja mwa Mwana wa Mulungu Yesu Khristu, amene ataukitsidwa kwa akufa, “anakhala pansi kudzanja lamanja la Mulungu. Kuyambila pamenepo, akuyembekezela kufikila pamene adani ake adzaikidwe monga copondapo mapazi ake.”—Aheb. 10:12, 13; Sal. 110:1; Chiv. 12:10.

DECEMBER 16-22

CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | CHIVUMBULUTSO 13-16

“Musamaope Zilombo Zoopsa”

w12 6/15 8 ¶6

Yehova Ndi “Woulula Zinsinsi”

Ca m’ma 96 C.E., Yesu woukitsidwayo anaonetsa mtumwi Yohane masomphenya osiyana-siyana odabwitsa kwambili. (Chiv. 1:1) Mu amodzi a masomphenyawo, Yohane anaona Mdyelekezi, ataimilidwa na cinjoka coimilila m’mbali mwa nyanja yaikulu. (Ŵelengani Chivumbulutso 13:1, 2.) Yohane anaonanso cilombo cachilendo cikutuluka m’nyanjayo ndipo Mdyelekezi anacipatsa ulamulilo waukulu. Kenako, mngelo anauzanso Yohane kuti mitu 7 ya cilombo cofiilaco, cimene ni cifanizilo ca cilombo ca pa Chivumbulutso 13:1, imaimila “mafumu 7,” kapena kuti maboma 7. (Chiv. 13:14, 15; 17:3, 9, 10) Pa nthawi imene Yohane analemba zimenezi, mafumu asanu anali atagwa kale, imodzi inalipo ndipo ‘inayo inali isanafikebe.’ Kodi mafumu kapena kuti maulamulilo amphamvu padziko lonse amenewa ndani? Tiyeni tikambilane za mutu uliwonse wa cilomboco cochulidwa m’buku la Chivumbulutso. Tionanso mmene ulosi wa Danieli ungatithandizile kudziŵa za mafumuwa. Ulosiwu unalembedwa kukali zaka zambili ena mwa mafumuwa asanakhaleko.

re 194 ¶26

Kulimbana na Zilombo Ziŵili Zoopsa

Kodi zikuimila ndani? Zikuimila ulamulilo wamphamvu kwambili padziko lonse wa Britain na America, umene uja woimilidwa na mutu wa namba 7 wa cilombo coyamba cija, koma apa ukucita mbali yapadela. Popeza kuti cilomboci acichula pacokha m’masomphenyawa, zikutithandiza kuona bwino mmene cikucitila zinthu pacokha m’dzikoli. Cilombo cophiphilitsila ca nyanga ziŵili cimeneci cikuimila maulamulilo andale aŵili olamulila pa nthawi imodzi m’maiko osiyana, koma akucita zinthu mogwilizana. Mfundo yakuti cili na nyanga ziŵili ngati za “mwana wa nkhosa,” ionetsa kuti cimadzionetsa ngati cofatsa komanso copanda nkhanza. Isonyezanso kuti cimadzionetsa ngati cimalamulila mokomela aliyense ndipo cimafuna kuti dziko lonse lizitsanzila ulamulilo wake. Koma cimalankhula ngati “cinjoka” cija. Izi zitanthauza kuti cimakakamiza anthu komanso kuwaopseza kuti avomeleze kalamulilidwe kake, ndipo ngati sakutelo cimawacitila zankhanza. Cilombo cimeneci sicilimbikitsa anthu kuti azigonjela Ufumu wa Mulungu umene wolamulila wake ni Mwanawankhosa wa Mulungu. M’malomwake, cimawalimbikitsa kuti azicita zofuna za Satana, cinjoka cacikulu cija. Cilombo ca nyanga ziwilici calimbikitsa kwambili mzimu wokonda dziko lako, umene wakulitsa cidani pakati pa anthu. Konseku n’kulambila cilombo coyamba cija.

re 195 ¶30-31

Kulimbana ndi Zilombo Ziŵili Zoopsa

Zimene zacitika m’mbili ya anthu zaonetsa kuti cifanizilo cimeneci ni bungwe limene maiko a Britain komanso United States ndiwo analikhazikitsa na kulicilikiza. Poyamba linali kudziŵika na dzina lakuti League of Nations. Kutsogoloku mu Chivumbulutso caputa 17, tiona cilombo cina coima pacokha, cofiila kwambili komanso camoyo, cimene cikuimilanso bungwe limeneli. Bungwe la padziko lonse limeneli ‘limalankhula,’ kutanthauza kuti limanena modzitama kuti ni bungwe lokhalo limene lingabweletse bata na mtendele kwa anthu. Koma kweni-kweni lakhala bwalo limene maiko amagwilitsila nchito pokangana na kunyozana. Bungweli limaopseza maiko kapena anthu amene sakugonjela ulamulilo wake, kuti lidzaleka kuwathandiza kapena liziwasala, kumene kuli ngati kuŵapha. Ndipotu bungweli linacotsa ndithu paumembala maiko amene sanali kutsatila mfundo zake. Ndipo cisautso cacikulu cikadzangoyamba, “nyanga” za cifanizilo ca cilomboci, zidzakwanilitsa mbali yake yocita nkhondo na kupha kwakukulu.—Chivumbulutso 7:14; 17:8, 16.

Kucokela pa nthawi ya nkhondo yaciŵili ya padziko lonse, cifanizilo ca cilomboci, cimene lomba ni United Nations, capha kale anthu ambili m’lingalilo leni-leni. Mwacitsanzo, mu 1950 asilikali a United Nations analoŵelela pa nkhondo ya pakati pa dziko la North Korea na South Korea. Asilikali a bungweli mogwilizana na asilikali a ku South Korea, anapha anthu pafu-pifupi 1,420,000 a ku North Korea komanso ku China. Ndiponso kuyambila mu 1960 mpaka mu 1964, asilikali a United Nations anamenya nawo nkhondo ya ku Democratic Republic of Congo. Ndipo atsogoleli ochuka m’dzikoli, kuphatikizapo Papa Paulo 6, na Papa Yohane Paulo 2, akhala akunena motsimikiza kuti cifanizilo cimeneci n’cokhaco cingabweletse mtendele kwa anthu. Iwo amanena motsimikiza kuti anthu akadzalephela kutumikila cifanizilo cimeneci, ndiye kudzakhala kutha kwa mtundu wa anthu. Conco mophiphilitsa iwo akucititsa kuti anthu onse amene akana kutsatila zofuna za cilomboco kapena kucilambila aziphedwa.—Deuteronomo 5:8, 9

w09 2/15 4 ¶2

Mfundo Zazikulu za m’Buku la Chivumbulutso—Gawo 2

13:16, 17. Ngakhale kuti umoyo wa tsiku na tsiku ni wovuta, monga “kugula kapena kugulitsa” zinthu, tisalole kuti cilomboci ciyambe kulamulila umoyo wathu. Tikacita zimenezo, ndiye kuti talola ‘cizindikilo ca cilomboco kulembedwa pa dzanja lathu kapena pamphumi pathu,’ na kucilola kulamulila zocita zathu na maganizo athu.

Kufufuza Cuma ca Kuuzimu

w09 2/15 4 ¶5

Mfundo Zazikulu za m’Buku la Chivumbulutso—Gawo 2

16:13-16. Mawu akuti “mauthenga . . . onyansa ouzilidwa” akutanthauza mabodza amene ziŵanda zikulimbikitsa, amene colinga n’cakuti mafumu a dziko lapansi aumitse capamutu posacita mantha na kukhuthulidwa kwa mbale zisanu na ziŵili za mkwiyo wa Mulungu. Kuti m’malomwake mafumuwo atukumuke mtima pofuna kulimbana na Yehova.—Mat. 24:42, 44.

w15 7/15 16 ¶9

“Cipulumutso Canu Cikuyandikila”

Nthawi imeneyi sidzakhala yolalikila ‘uthenga wabwino wa ufumu.’ Nthawi yolalikila idzakhala itatha kale cifukwa “mapeto” adzakhala atafika. (Mat. 24:14) Anthu a Yehova pa nthawiyo adzalengeza uthenga woopsa waciweluzo. N’kutheka kuti adzalengezanso za kufika kwa mapeto othelatu dziko Satana loipali. Baibo imayelekezela uthenga umenewu na matalala aakulu. Limakamba kuti: “Matalala aakulu, lililonse lolemela pafu-pifupi makilogalamu 20, anagwela anthu kucokela kumwamba. Anthuwo ananyoza Mulungu cifukwa ca mlili wa matalalawo, pakuti mliliwo unali waukulu modabwitsa.”—Chiv. 16:21.

DECEMBER 23-29

CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | CHIVUMBULUTSO 17-19

“Nkhondo ya Mulungu Idzathetsa Nkhondo Zonse”

w08 4/1 8 ¶3-4

Aramagedo Nkhondo ya Mulungu Yothetsa Nkhondo Zonse

Malinga ngati ulamulilo uli m’manja mwa anthu oipa, anthu olungama sangaone bata na mtendele. (Miyambo 29:2; Mlaliki 8:9) N’zosatheka kupeza cilungamo kwa anthu ocita zoipa. Conco, kuti pakhale mtendele weni-weni na cilungamo, anthu oipa adzafunika kucotsedwapo coyamba. N’cifukwa cake Solomo analemba kuti: “Wocimwa ndiye ciombolo ca wolungama.”—Miyambo 21:18.

Popeza Mulungu ndiye Woweluza, tikhulupilila kuti adzaweluza mwacilungamo mlandu uliwonse wokhudza anthu ocimwa. N’cifukwa cake Abulahamu anafunsa kuti: “Kodi sadzacita zoyenela Woweluza wa dziko lonse lapansi?” Yankho limene anapeza n’lakuti Yehova amacita zolungama nthawi zonse. (Genesis 18:25) Komanso, Baibo imatitsimikizila kuti Yehova sakondwela powononga anthu oipa. Amangotelo cifukwa cokana kwawo kusintha.—Ezekieli 18:32; 2 Petulo 3:9.

it-1 1146 ¶1

Hosi

M’masomphenya ophiphilitsila a mtumwi Yohane, iye anaona Yesu Khristu waulemelelo atakwela hosi yoyela ndipo gulu la asilikali linali kumutsatila, onse atakwela pa mahosi oyela. Yohane anauzidwa kuti masomphenyawo akuonetsa nkhondo yacilungamo imene Khristu adzamenya powononga adani a Atate wake komanso Mulungu wake, Yehova. (Chiv. 19:11, 14) Kuciyambi, zimene Khristu anacita monga mfumu, komanso matsoka amene anatsatilapo, zikuimilidwa na amuna okwela pa mahosi osiyana.—Chiv. 6:2-8.

re 286 ¶24

Mfumu Yankhondo Idzapambana pa Aramagedo

Cilombo ca mitu 7 na nyanga 10 cotuluka m’nyanja, cimene cikuimila maulamulilo andale amene Satana wakhazikitsa, cidzawonongedwa pamodzi na mneneli wonyenga uja, amene akuimila ulamulilo wa namba 7 wamphamvu kwambili padziko lonse. (Chivumbulutso 13:1, 11-13; 16:13) Cilomboci komanso mneneli wonyengayu adzaponyedwa “m’nyanja ya moto” akali “amoyo,” kapena kuti akucitabe zinthu mogwilizana, potsutsana ndi anthu a Mulungu padziko lapansi. Kodi nyanja ya motoyi ni nyanja yeni-yeni? Ayi ni yophiphilitsila, monga mmene cilomboco komanso mneneli wonyengayu alili wophiphilitsanso. Conco nyanja ya motoyo ikuimila ciwonongeko cothelatu comwenso ni comaliza, kutanthauza kuti owonongedwawo sadzakhalaponso konse. N’cifukwa cake pamapeto pake imfa na Manda, komanso Mdyelekezi weni-weniyo adzaponyedwa m’nyanja imeneyi. (Chivumbulutso 20:10, 14) Conco nyanja imeneyi si ng’anjo ya moto weni-weni, kumene anthu ena amaganiza kuti anthu oipa amakazunzika kwamuyaya. Zimenezi si zoona cifukwa Yehova amanyansidwa na ciphunzitso cakuti anthu oipa amakazunzika kwamuyaya m’ng’anjo ya moto.—Yeremiya 19:5; 32:35; 1 Yohane 4:8, 16.

re 286 ¶25

Mfumu Yankhondo Idzapambana pa Aramagedo

Ena onse amene sali m’gulu la olamulila andale, koma okhalabe ku mbali ya dziko loipa limene silingathe kusintha, nawonso ‘adzaphedwa na lupanga lalitali la wokwela pahaci.’ Yesu adzawaweluza monga oyenela kuphedwa. Popeza kuti Baibo siinena kuti anthu amenewa adzaponyedwa m’nyanja ya moto, kodi tingayembekezele kuti adzaukitsidwa? Mawu a Mulungu sanena pena paliponse kuti anthu amene adzaphedwe pa nthawi imeneyo ndi Woweluza woikidwa na Yehova, adzaukitsidwa. Monga mmene Yesu anakambila, onse amene si “nkhosa” adzacoka kupita “kumoto wosatha wokolezedwela Mdyelekezi ndi angelo ake,” kutanthauza kuti adzapita ku “ciwonongeko cothelatu.” (Mateyu 25:33, 41, 46) Ndico cidzakhala cimake ca ‘tsiku laciweluzo na ciwonongeko ca anthu osaopa Mulungu.’—2 Petulo 3:7; Nahumu 1:2, 7-9; Malaki 4:1.

Kufufuza Cuma ca Kuuzimu

re 247-248 ¶5-6

Cinsinsi Cocititsa Mantha Cinaululika

‘Cilombo cija cinalipo,’ kutanthauza bungwe la League of Nations, kuyambila pa January 10, 1920 kupita kutsogolo, ndipo maiko amene anakhalapo m’bungweli anali okwana 63. Koma motsatizanatsatizana, maiko a Japan, Germany na Italy anacoka m’bungweli, ndiponso dziko limene kale linali Soviet Union linacotsedwamo. Mu September 1939, wolamulila wankhanza wa cipani ca Nazi ku Germany anayambitsa nkhondo yachiŵili ya padziko lonse. Bungwe la League of Nations linalephela kukhazikitsa mtendele padziko lapansi. Conco linatha nchito moti linangokhala ngati laponyedwa kuphompho. Pofika mu 1942 bungweli linali lisakugwilanso nchito. Pa nthawi yoyenelela imeneyi, osati pa nthawi ya m’mbuyo kapena pa nthawi ina yake m’tsogolo, Yehova anaululila anthu ake tanthauzo lonse la masomphenyawa. Pamsonkhano wakuti “Dziko Latsopano Lolamulidwa ndi Mulungu,” N. H. Knorr ananena mogwilizana na ulosi umenewu kuti ‘cilombo cija tsopano palibe.’ Kenako iye anafunsa kuti, “Kodi bungwe la League of Nations lidzakhala kuphompho mpaka kalekale?” Poyankha, iye anagwila mawu a pa Chivumbulutso 17:8, ndipo anati: “Bungwe loimila mgwilizano wa maiko lidzayambilanso.” Zimenezi zinacitikadi, ndipo zinaonetsa kuti Mawu a ulosi a Yehova ni oona.

Cinatuluka Kuphompho

Cilombo cofiila kwambili cija cinatulukadi kuphompho. Pa June 26, 1945, maiko 50 anavota kuvomeleza cigamulo cokhazikitsila bungwe la United Nations. Zimenezi zinacitika ku San Francisco, m’dziko la United States, pa mwambo umene panali cisangalalo cacikulu kwambili. Colinga ca bungwe latsopanoli cinali “kukhazikitsa bata ndi mtendele padziko lonse.” Bungwe la United Nations linafanana kwambili na bungwe la League of Nations. Buku lina linati: “Bungwe la United Nations (UN) limafanana m’njila zina na bungwe la League of Nations, limene linakhazikitsidwa nkhondo yoyamba ya padziko lonse itatha . . . Mwacitsanzo, maiko ambili amene anayambitsa bungwe la UN ni amenenso anayambitsa bungwe la League of Nations. Mofanana na bungwe la League of Nations, bungwe la UN linakhazikitsidwa kuti lizithandiza kukhazikitsa mtendele pakati pa maiko. Ndipo nthambi zikulu-zikulu za UN n’zofanana ndi za League of Nations.” (The World Book Encyclopedia) Conco, bungwe la UN likuimila cilombo cofiila kwambili cimene cinatuluka kuphompho. M’bungweli muli maiko pafupi-fupi 192 ndipo akuposa maiko 63 amene anali mu League of Nations. Komanso bungweli limagwila nchito zambili kuposa bungwe la League of Nations.

w12 6/15 18 ¶17

Yehova Avumbula “Zimene Ziyenela Kucitika Posacedwapa”

Koma zipembedzo zonyenga sizidzangozimililika zokha. Hule imeneyo idzapitiliza kukhala yamphamvu ndiponso kuyesetsa kukopa mafumu mpaka pamene Mulungu adzaika maganizo ena m’mitima ya mafumuwo. (Ŵelengani Chivumbulutso 17:16, 17.) Posacedwapa, Yehova adzapangitsa magulu andale a dziko la Satanali, amene akuimilidwa na bungwe la United Nations, kuti aukile zipembedzo zonyenga. Iwo adzathetsa mphamvu zake na kusakaza cuma cake. Zaka zocepa zapitazo, anthu sakanakhulupilila kuti zimenezi zingacitike. Koma masiku ano, huleyi ili pendapenda pamsana wa cilombo cofiila kwambili. Ngakhale zili conco, siidzagwa pang’onopang’ono, koma idzagwetsedwa mwadzidzidzi ndiponso mwamphamvu.—Chiv. 18:7, 8, 15-19.

DECEMBER 30–JANUARY 5

CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | CHIVUMBULUTSO 20-22

“Taonani! Zinthu Zonse Zimene Ndikupanga N’zatsopano”

re 301 ¶2

Kumwamba Kwatsopano ndi Dziko Lapansi Latsopano

Zaka mahandiledi kumbuyoku nthawi ya Yohane isanafike, Yehova anauza Yesaya kuti: “Pakuti ndikulenga kumwamba kwatsopano ndi dziko lapansi latsopano. Zinthu zakale sizidzakumbukilidwanso ndipo sizidzabwelanso mumtima.” (Yesaya 65:17; 66:22) Ulosi umenewu unakwanilitsidwa koyamba pamene Ayuda okhulupilika anabwelela ku Yerusalemu mu 537 B.C.E., atakhala zaka 70 mu ukapolo ku Babulo. Iwo atabwelela kwawo, anakhala mtundu woyela, kapena kuti “dziko lapansi latsopano,” ndipo anali na ulamulilo watsopano, kapena kuti “kumwamba kwatsopano.” Komabe, mtumwi Petulo anaonetsa kuti ulosiwu udzakwanilitsidwanso mwanjila ina pamene anati: “Koma pali kumwamba kwatsopano ndi dziko lapansi latsopano zimene ife tikuyembekezela mogwilizana ndi lonjezo lake, ndipo mmenemo mudzakhala cilungamo.” (2 Petulo 3:13) Tsopano Yohane anaonetsa kuti lonjezo limeneli likukwanilitsidwa m’tsiku la Ambuye. “Kumwamba kwakale ndi dziko lapansi lakale,” zidzacoka. Zimenezi zikuimila dziko la Satanali pamodzi na maboma ake olamulila, amene amacita zinthu motsogoleledwa na Satana pamodzi na ziwanda zake. “Nyanja” yamafunde, imene ikuimila anthu oipa komanso osamvela Mulungu, sidzakhalaponso. Zinthu zimenezi zidzalowedwa m’malo ndi “kumwamba kwatsopano ndi dziko lapansi latsopano,” zimene zikuimila mtundu watsopano wa anthu okhala padziko lapansi amene adzalamulilidwa na boma latsopano, limene ni Ufumu wa Mulungu.—Yelekezelani ndi Chivumbulutso 20:11.

w13 12/1 11 ¶2-4

“Taonani! Zinthu Zonse Zimene Ndikupanga N’zatsopano”

“[Mulungu] adzapukuta misozi yonse m’maso mwawo.” (Chivumbulutso 21:4) Kodi ni misozi iti imene iye adzapukuta? Mulungu sadzapukuta misozi ya cisangalalo kapena misozi imene imateteza maso athu. Adzapukuta misozi yobwela cifukwa ca mavuto ndiponso kulila. Mulungu adzapukuta misozi kothelatu mwa kucotsa mavuto na zopweteka zimene zimapangitsa anthu kugwetsa misozi.

“Imfa sidzakhalaponso.” (Chivumbulutso 21:4) Palibe cinthu cina cimene capangitsa anthu kugwetsa misozi kuposa mdani wathu imfa. Yehova adzapulumutsa anthu omvela ku imfa. Kodi adzacita bwanji zimenezi? Adzacotselatu ucimo wocokela kwa Adamu umene unayambitsa imfa. (Aroma 5:12) Yehova adzabwezeletsa anthu omvela ku ungwilo kudzela m’nsembe ya dipo la Yesu. Ndiyeno mdani womalizila, imfa, “adzawonongedwa.” (1 Akorinto 15:26) Cotelo, anthu okhulupilika adzakhala na moyo wathanzi kwamuyaya, monga mmene Mulungu anafunila.

“Sipadzakhalanso . . . kupweteka.” (Chivumbulutso 21:4) Kodi ni kupweteka kotani kumene sikudzakhalakonso? Sikudzakhala kuvutika maganizo, nkhawa kapena zopweteka zina m’thupi, zobwela cifukwa ca ucimo na kupanda ungwilo kumene kumavutitsa anthu mamiliyoni ambili.

w03 8/1 12 ¶14

Yehova, Mulungu wa Coonadi

Tiyenela kukhulupilila zimene Yehova amatiuza m’Mawu ake. Mmene iye amadzifotokozela na mmene alilidi, ndipo adzacitadi zimene amanena. Palibe cifukwa coti tisakhulupilile Mulungu. Tiyenela kukhulupilila pamene Yehova anena kuti adzabweletsa “cilango kwa iwo osam’dziŵa Mulungu, na iwo osamvela Uthenga Wabwino wa Ambuye wathu Yesu.” (2 Atesalonika 1:8) Tiyenelanso kum’khulupilila Yehova pamene anena kuti amakonda anthu ocita cilungamo, pamene anena kuti adzapeleka moyo wosatha kwa anthu amene amacita zinthu zoonetsa kuti ali na cikhulupililo, ndiponso pamene anena kuti adzacotsa kupweteka, kulila, ngakhale imfa. Yehova anatsimikizila kuti lonjezo lomalizali n’lodalilikadi mwa kulangiza mtumwi Yohane kuti: “Talemba; pakuti mawu awa ali okhulupilika ndi oona.”—Chivumbulutso 21:4, 5; Miyambo 15:9; Yohane 3:36.

Kufufuza Cuma ca Kuuzimu

it-2 249 ¶2

Moyo

M’lamulo limene Mulungu anapatsa Adamu, anaonetsa kuti ngati Adamu adzamvela sadzafa. (Gen. 2:17) Conco, mdani wotsiliza wa anthu, imfa, akakawonongedwa, anthu omvela sadzakhalanso na ucimo, umene umabweletsa imfa. Sudzagwilanso nchito m’matupi awo. Iwo sadzafa mpaka muyaya. (1 Akor. 15:26) Imfa idzawonongedwa kumapeto kwa ulamulilo wa Khristu, umene buku la Chivumbulutso limaonetsa kuti udzatenga zaka 1,000. Baibo imakamba kuti anthu amene adzakhala mafumu komanso ansembe pamodzi na Khristu, “anakhalanso ndi moyo ndipo analamulila monga mafumu limodzi ndi Khristu zaka 1,000.” “Akufa enawo” amene sadzakhalanso na moyo “kufikila zitatha zaka 1,000” ayenela kuti ni aja amene adzakhala ali moyo kumapeto kwa zaka 1,000, Satana asanamasulidwe ku phompho kuti ayese anthu komaliza. Pakutha kwa zaka 1,000, anthu padziko adzakhala angwilo monga mmene Adamu na Hava anali asanacimwe. Panthawiyo, m’pamene adzakhala na moyo weni-weni wangwilo. Awo amene adzapyola ciyeso cotsiliza pamene Satana adzamasulidwa ku phompho kwa kanthawi kocepa, adzakondwela na moyo wosatha.—Chiv. 20:4-10.

it-2 189-190

Nyanja ya Moto

Mawu amenewa amapezeka cabe m’buku la Chivumbulutso, ndipo mwacionekele ni ophiphilitsila. Baibo imatifotokozela zimene mawuwa amaphiphilitsila. Imati: “Nyanja yamoto imeneyi ikuimila imfa yaciŵili.”—Chiv. 20:14; 21:8.

Zimene nyanja yamoto ikuphiphilitsila, zikuonekelanso bwino m’mavesi ena a m’buku la Chivumbulutso. Imfa ikufotokozedwa kuti inaponyedwa m’nyanja ya moto. (Chiv. 19:20; 20:14) N’zodziŵikilatu kuti imfa yeni-yeni singatenthedwe na moto. Cinanso, Mdyelekezi amene ni colengedwa ca mzimu, akufotokozedwa kuti anaponyedwa m’nyanja ya moto. Popeza ni mzimu, iye sangatenthedwe na moto.—Chiv. 20:10; yelekezelani na Eks. 3:2 na Ower. 13:20.

Popeza nyanja ya moto ikuimila “imfa yaciŵili,” ndipo pa Chivumbulutso 20:14 pamakamba kuti zonse “imfa ndi Manda” zidzaponyedwa mu nyanjayi, n’zoonekelatu kuti nyanja imeneyi siingaimile imfa imene anthu anatengela kwa Adamu (Aroma 5:12) kapena Manda (Sheol). Conco, nyanjayi imaphiphilitsila mtundu wina wa imfa imene ilibe ciyembekezo cokhalanso na moyo, cifukwa palibe paliponse pamene pamakamba kuti “nyanja yamoto” idzapeleka amene ali mmenemo, monga mmene imfa yocokela kwa Adamu na Manda (Sheol) zidzacitila zimenezo. (Chiv. 20:13) Conco, anthu amene maina awo sanalembedwe “m’buku la moyo,” osalapa amene amatsutsa ulamulilo wa Mulungu, adzaponyedwa m’nyanja ya moto, kutanthauza ciwonongeko ca muyaya, kapena kuti imfa yaciŵili.—Chiv. 20:15.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani