UMOYO WATHU WACIKHRISTU
Mmene Mwamuna na Mkazi Wake Angalimbitsile Cikwati Cawo
Abulahamu na Sara anali citsanzo cabwino monga mwamuna na mkazi wake amene anali kukondana na kulemekezana. (Gen. 12:11-13; 1 Pet. 3:6) Ngakhale n’conco, cikwati cawo sicinali cangwilo, anafunika kupilila mayeselo mu umoyo wawo. Kodi okwatilana angaphunzile ciani pa citsanzo ca Abulahamu na Sara?
Muzikambilana. Yankhani modekha ngati mnzanu wa m’cikwati akukamba motaya mtima kapena mokhumudwa. (Gen. 16:5, 6) Muzipatula nthawi yocezela pamodzi. Mwa mawu na zocita zanu, onetsani mnzanuyo kuti mumam’konda. Koposa zonse, ikani Yehova patsogolo m’cikwati canu. Citani izi mwa kuŵelengela pamodzi, kupemphela, komanso kulambilila pamodzi. (Mlaliki 4:12) Zikwati zolimba zimalemekeza Yehova, amene anakhazikitsa makonzedwe opatulika amenewa.
TAMBITSANI VIDIYO YAKUTI ZIMENE MUNGACITE KUTI MULIMBITSE CIKWATI CANU, NDIYENO YANKHANI MAFUNSO AYA:
Mu vidiyoyi, mwaona zizindikilo zotani zoonetsa kuti Shaan na Kiara anayamba kutalikilana?
N’cifukwa ciani kukambilana momasuka komanso moona mtima n’kofunika m’cikwati?
Kodi citsanzo ca Abulahamu na Sara cinathandiza bwanji Shaan na Kiara?
Kodi Shaan na Kiara anatenga masitepu ati kuti alimbitse cikwati cawo?
N’cifukwa ciani mwamuna na mkazi wake sayenela kuyembekezela ungwilo m’cikwati cawo?
N’zotheka ndithu kulimbitsa cikwati canu!