LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • mwb21 January tsa. 5
  • Tetezani Cikwati Canu

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Tetezani Cikwati Canu
  • Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2021
  • Nkhani Zofanana
  • Kupangitsa Cikwati Cacikhiristu Kukhala Cacimwemwe
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2016
  • Pambuyo Pa Tsiku La Cikwati
    Mmene Tingakhalilebe mu Cikondi ca Mulungu
  • Kuyankha Mafunso a M’baibo
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2013
  • ‘Cikwati Cikhale Colemekezeka’
    “Khalanibe m’Cikondi ca Mulungu”
Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2021
mwb21 January tsa. 5
Mwamuna wakhala pansi pafupi na mkazi wake, ndipo akuwachila limodzi zovala mwacimwemwe.

UMOYO WATHU WACIKHRISTU

Tetezani Cikwati Canu

Yehova amaona kuti malumbilo a cikwati ni nkhani yaikulu. Iye anakamba kuti mwamuna na mkazi wake afunika kukhala limodzi osalekana. (Mat. 19:5, 6) Pakati pa anthu a Mulungu pali ambili amene ali na vikwati vabwino. Ngakhale n’conco, kulibe cikwati cangwilo. Banja lililonse limakumana na mavuto. Conco tiyenela kupewa maganizo amene anthu ambili m’dzikoli ali nawo akuti kupatukana na kusudzulana ndiwo mankhwala othetsela mavuto m’cikwati. Kodi mabanja acikhristu angateteze bwanji cikwati cawo?

Onani mfundo zisanu izi zofunika.

  1. Tetezani mtima wanu mwa kupewa zinthu monga kuceza mokopana komanso zosangalatsa zolimbikitsa ciwelewele zimene zingathe kusokoneza cikwati.—Mat. 5:28; 2 Pet. 2:14.

  2. Limbitsani ubwenzi wanu na Mulungu, ndipo kulitsani mtima wofuna kum’kondweletsa m’cikwati canu.—Sal. 97:10.

  3. Pitilizani kuvala umunthu watsopano, ndipo muzicitila mnzanu wa m’cikwati ngakhale zinthu zocepa cabe zoonetsa kukoma mtima kuti mum’kondweletse.—Akol. 3:8-10, 12-14.

  4. Muzikambilana mwaulemu na moona mtima. —Akol. 4:6.

  5. Muzipeleka mangawa a m’ciwati mwacikondi. —1 Akor. 7:3, 4; 10:24.

Akhristu akamalemekeza cikwati, ndiye kuti akulemekeza Yehova amene ni Woyambitsa cikwati.

ONETSANI VIDIYO YAKUTI TIFUNIKA ‘KUTHAMANGA MOPILILA’—TSATILANI MALANGIZO A MPIKISANO, NDIYENO YANKHANI MAFUNSO OTSATILAWA:

  • Zocitika za mu vidiyo yakuti ‘Tifunika ‘Kuthamanga Mopilila’—Tsatilani Malangizo a Mpikisano.’ M’bale na Mlongo Calou akumwetulila pambuyo pa nkhani ya cikwati cawo mu Nyumba ya Ufumu.

    Ngakhale kuti cikwati cingakhale na ciyambi cabwino, ni mavuto ati amene angabuke?

  • Zocitika za mu vidiyo yakuti ‘Tifunika ‘Kuthamanga Mopilila’—Tsatilani Malangizo a Mpikisano.’ M’bale na Mlongo Calou akukambilana mavuto awo modekha, ndipo Baibo yotsegula ili pa thebulo.

    Kodi mfundo za m’Baibo zingawathandize bwanji anthu amene amaona kuti sakondedwa m’cikwati?

  • Zocitika za mu vidiyo yakuti ‘Tifunika ‘Kuthamanga Mopilila’—Tsatilani Malangizo a Mpikisano.’ M’bale Calou akuŵelengela mkazi wake na ana awo aŵili aakazi buku lakuti, ‘Buku Langa la Nkhani za M’Baibo.’

    Seŵenzetsani mfundo za m’Baibo kuti mukhale acimwemwe m’cikwati canu

    Kodi Yehova anaika malamulo otani m’cikwati?

  • Kuti cikwati ciziyenda bwino, kodi mwamuna na mkazi wake ayenela kucita ciani?

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani