June 15-21
GENESIS 48-50
Nyimbo 30 na Pemphelo
Mawu Oyamba (1 min.)
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
“Acikulile Ali na Zambili Zotiphunzitsa”: (10 min.)
Gen. 48:21, 22—Yakobo anaonetsa cikhulupililo cakuti kutsogolo dziko la Kanani lidzagonjetsedwa (it-1 1246 ¶8)
Gen. 49:1—Ulosi umene Yakobo anakamba ali pafupi kufa unaonetsa cikhulupililo cake (it-2 206 ¶1)
Gen. 50:24, 25—Yosefe anali na cikhulupililo cakuti malonjezo a Yehova adzakwanilitsidwa (w07 6/1 28 ¶10)
Kufufuza Cuma ca Kuuzimu: (10 min.)
Gen. 49:19—Kodi ulosi umene Yakobo analosela ponena za Gadi unakwanilitsidwa bwanji? (w04 6/1 15 ¶4-5)
Gen. 49:27—Kodi ulosi umene Yakobo analosela ponena za Benjamini unakwanilitsidwa bwanji? (it-1 289 ¶2)
Pa kuŵelenga Baibo kwa wiki ino, ni mfundo yopindulitsa iti imene munapeza yokhudza Yehova Mulungu, ulaliki, kapena mfundo ina iliyonse?
Kuŵelenga Baibo: (4 min. olo kucepelapo) Gen. 49:8-26 (th phunzilo 5)
CITANI KHAMA PA ULALIKI
Vidiyo ya Ulendo Wobwelelako: (5 min.) Kukambilana. Tambitsani vidiyoyi, ndiyeno funsani omvetsela mafunso otsatilawa: Kodi ofalitsa aja athandizana bwanji polalikila? Nanga tingatengele bwanji citsanzo cawo pankhani yolankhula mwacidalilo polalikila?
Ulendo Wobwelelako: (3 min. olo kucepelapo) Mukayamba makambilano acitsanzo, mwininyumba akambe mawu ofala kwanuko amene anthu amakamba pofuna kukana kuwalalikila. Koma muyankheni mwaluso. (th phunzilo 6)
Ulendo Wobwelelako: (5 min. olo kucepelapo) Yambani na makambilano acitsanzo. Ndiyeno gaŵilani buku lakuti Zimene Baibulo Ingatiphunzitse, kenako yambitsani phunzilo la Baibo m’mutu 9. (th phunzilo 16)
UMOYO WATHU WACIKHRISTU
“Kodi Mungaphunzile Ciani kwa Akhristu Amene ni Aciyambakale?” (15 min.) Kukambilana. Tambitsani vidiyo yakuti Kusunga Mgwilizano pa Nthawi ya Ciletso.
Phunzilo la Baibo la Mpingo: (30 min.) jy mutu 119
Mawu Othela (3 min. olo kucepelapo)
Nyimbo 25 na Pemphelo