LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • mwb20 July tsa. 7
  • Yehova Amateteza Anthu Ake

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Yehova Amateteza Anthu Ake
  • Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2020
  • Nkhani Zofanana
  • Kodi Baibulo Limakamba Ciani?
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila)—2016
  • Kodi Mumaona “Wosaonekayo”?
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2014
  • Miziyamu ya Mabaibo ku Nthambi ya Belgium Imaonetsa Zimene Anthu Anacita Poteteza Mawu a Mulungu
    Nkhani Zina
  • Musaleke Kutsatila Citsogozo ca Yehova
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2024
Onaninso Zina
Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2020
mwb20 July tsa. 7

UMOYO WATHU WACIKHRISTU

Yehova Amateteza Anthu Ake

Tate waciisiraeli na mwana wake akuwaza magazi pa mafelemu a nyumba yawo.

Mwambo woyamba wa Pasika unali cocitika cofunika kwambili. Tsiku lina usiku, pambuyo pakuti Farao waona kuti mwana wake woyamba kubadwa waphedwa, anauza Mose kuti: “Nyamukani, cokani pakati pa anthu anga, inuyo ndi ana onse a Isiraeli. Pitani, katumikileni Yehova, monga momwe mwanenela.” (Eks. 12:31) Yehova anaonetsa kuti amateteza anthu ake.

Tikaona mbili yamakono ya anthu a Yehova, n’zoonekelatu kuti Yehova wapitiliza kuwatsogolela na kuwateteza. Izi zionekela bwino mu miziyamu yathu yochedwa “Anthu Odziŵika na Dzina la Yehova,” imene ili ku likulu lathu la padziko lonse.

TAMBITSANI VIDIYO YAKUTI KUYENDELA MIZIYAMU YA KU WARWICK: “ANTHU ODZIŴIKA NA DZINA LA YEHOVA,” NDIYENO YANKHANI MAFUNSO OTSALIWA:

  • Cikwangwani na zithunzi za mu ‘Sewelo la Pakanema la Cilengedwe.’

    Kodi ni zida ziti zimene Ophunzila Baibo anayamba kuseŵenzetsa mu 1914, polimbikitsa cikhulupililo cawo pa Baibo? Nanga panali zotulukapo zotani?

  • Tumapikica twa abale amene anagwidwa na kuikidwa mndende mu 1918.

    Kodi ni zopinga zotani zimene anakumana nazo mu 1916 komanso mu 1918? Nanga panali umboni wotani woonetsa kuti Yehova anali kutsogolela gulu lake?

  • Cithunzi mu myuziyamu coonetsa abale ambili amene anamangidwa cifukwa ca cikhulupililo cawo. Zitseko zolowela m’cipinda mmene muli cithunzi coonetsa Paladaiso.

    Kodi anthu a Yehova amacilimika bwanji pa cikhulupililo cawo pamene anthu ena awatsutsa?

  •  Cithunzi mu myuziyamu coonetsa njila zina zolalikila zimene zinali kuseŵenzetsedwa m’ma 1930 na 1940.

    Kodi ni kamvedwe katsopano kati kamene anthu a Yehova analandila mu 1935? Nanga zimenezi zinawakhudza bwanji?

  • Ngati munayendako kukaona miziyamu imeneyi, kodi n’ciani cimene munaona cimene cinalimbitsa cikhulupililo canu cakuti Yehova amatsogolela na kuteteza anthu ake?

Kuti mudziŵe zimene mungacite kuti mukaoneko miziyamu imeneyi, pitani pa jw.org® na kuloŵa pa mbali yakuti Zokhudza Ife

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2026)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani